Bambo wina ku Zomba yemwe dzina lake ndi Ronnex Bandawe wapezeka olakwa pa mlandu oti adawotcha dzanja la mwana wa zaka zisanu ndi chimodzi (6) yemwe ndi mwana wachemwali wabamboyu ati chifukwa adaba chimanga chimodzi.
Pakali pano oweruza mlandu Christopher Makumba akuyembekedzeka kudzapereka chigamulo chake pa 18 April mwezi uno.
Bungwe la Development Communications Trust (DCT) ndilomwe lidakonza kuti mulandu wa Ronnex Bandawe ukakambidwe kwa Senior Chief Chikowi.
DCT yati ikufuna kuti milandu ina yawupandu idzikakambidwa kumadera akumudzi (mobile courts) pofuna kuti anthu adzidziwa momwe milandu imakambiridwa kumabwalo amilandu komanso anthu ena adzitengerapo phunziro.
Woyendetsa mapologalamu ku DCT a Bettie Chumbu ati kutengera milandu yawupandu monga yochitirana nkhanza m’banja komanso yogwilira ana kumadera akumudzi kupangitsa kuti milandu idzichepa komanso zipangitsa kuti anthu omwe amakhala ndi mtima wofuna kupalamula milandu yawupandu adzichita mantha.
Pamenepa iye wati pomwe Bungwe lake la DCT lathandizira kuti mulandu wa Ronnex Bandawe ukakambidwe kumudzi komwe kumakhala anthu alandira milandu yopitilira khumi yofuna kuti ikakambidwe kumadera akumudzi.
“Tipemphe anzathu okonza malamulo kuti atithandidzire kupanga support ma mobile courts services pofuna kuti milandu yawupandu idzikaneneredwa kumudzi.” Adatero Bettie Chumbu.
Mu mau ake wapampando wa achinyamata mdera la Senior Chief Chikowi Wongani Chawinga wati kubwera kwa khoti loyendera mdelaro kupangitsa kuti nkhanza zomwe achinyamata komanso ana amakumana nazo zichepa tsopano anthu azichita mantha.
Chawinga wati pakali pano ayetsetsa kuti achiyamata amdera la Senior Chief Chikowi adzigwira ntchito limodzi ndi apolisi pofuna kuwonetsetsa kuti nkhadza za achinyamata zichepe.
Follow us on Twitter: