Chakwera wakhululukira Mussa John

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wakhululukira Mussa John yemwe chaka chatha analamulidwa kukakhala ku ndende kwa zaka zitatu atapezeka olakwa pa mlandu opezeka ndi chamba.

Nduna ya za mdziko a Zikhale Ng’oma atsimikiza kuti John ndi m’modzi wa akaidi 200 omwe akhululukidwa potengera nyengo ino yokumbukira kufa ndi kuuka kwa Ambuye Yesu.

John anapezeka ndi chamba chaka chatha ku Blantyre ndipo khothi la majisitileti linalamula kuti akaseve ukaidi kwa zaka zisanu ndi zitatu.

Anthu ambiri anaonetsa kukhumudwa ndi chilango chokhwimachi ndipo maloya atakamang’ala ku bwalo lalikulu chilango cha John chinachepetsedwa kuti akakhale ku ndende zaka zitatu.  

A Chakwera akhululukiranso a Uladi Mussa omwe mu 2020 anagamulidwa kukakhala ku ndende zaka zisanu chifukwa chopereka unzika mwa chinyengo  kwa anthu omwe si a Malawi. A Uladi anachita izi pomwe anali induna ya za mdziko.

Ena omwe a Chakwera awatulutsa ndi Jones Tewesa omwe anali dalaivala wa Linda Kunje yemwe ndi komishonala wakale wa bungwe la zisankho la MEC.

A Tewesa chaka chatha anawagamula kuti akakhale ku ndende kwa miyezi 18 atapezeka olakwa pa mlandu osokoneza mdipiti wa a Chakwera. A Tewesa anawagamula limodzi ndi a Kunje koma a Kunje anakhululukidwa kale chaka chatha mu December.

Akaidi ena omwe akhululukidwa ndi omwe anapalamula milandu ing’onoin’gono, malingana ndi a Ng’oma.

Mu nyengo ngati yomweyi chaka chatha a Chakwera anatulutsa akaidi 106. Chikhalireni pa mpando wa upulezidenti, a Chakwera atulutsa akaidi okwana 1900.

Advertisement