Achibale afukula manda a m’bale wawo ku Machinjiri

Advertisement

Kunali chipwilikiti kwa Jumbe ku Makhetha mdera la Machinjiri mumzinda wa Blantyre pomwe anthu Lolemba anafukula manda a m’bale wawo poganizira kuti anthu ena anaba bokosi lomwe anamuikamo.

Nkhaniyi ikutsatira mphekesera zomwe zakhala zikuveka kudelari kuti anthu ena achipongwe anafukula ndikuba bokosi la malemu Olive Balakasi omwe anamwalira kumayambiliro achaka chino ndipo thupi lawo lina lowa mmanda pa 3 January.

Chinatsitsa dzaye mchakuti manda a malemuwa anapezeka kuti akhuvukira zomwe zinapangitsa kuti anthu ayambe kufalitsa nkhani yoti bokosilo labedwa zomwe sizinasangalatse achibale komaso anasi ena a malemuwa.

Podziwa kuti kutsutsa galu mkukumba, Lolemba pa 23 January, achibale pamodzi ndi anthu ena anakhamukira ku manda a kwa Jumbe ku Machinjiri komwe anayamba kufukula malo omwe mai Balakasi anaikidwa kuti awone ngati mphekeserazo zinali zowona kapena zabodza.

Koma motsutsana ndimaganizo a anthuwa, ofukulawo anapeza kuti bokosilo lili mchimake silinabedwe zomwe zinapangitsa kuti omwe amafalitsa nkhaniyi agwidwe kakasi.

Zitatele, anthuwa anayambiraso kukwilira mandawo kenako onse ananyamuka mkumabwelera mmakwawo kwinaku manja ali kunkhongo ndipo pakadali pano bata labwelera kudelari.

Follow us on Twitter:

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.