Wobadwa ndi ziwalo zobisika ziwiri akupempha thandizo

Advertisement

…akufuna madotolo kunja akamudule chiwalo chachimuna

Wachisodzera wa zaka 21 yemwe anabadwa ndichiwalo chachikazi komaso chachimuna, wapempha anthu akufuna kwabwino kuti amuthandize kuti apite kunja kuti akamudule chiwalo chachimuna chomwe akuti chikumuzuza kwambiri.

Wachisodzerayu yemwe munkhani ino timutchule kuti Mphatso, amayankhula izi pomwe amacheza ndi Rodwell Lumbe yemwe amachita utolankhani wa nzika ndipo wakhala akupangitsa mapologalamu otchedwa ‘The Citizen Talk Show’.

Koma munthu mkumafusa kuti kodi zinakhala bwanji? Mphatso yemwe ukamuyang’ana thupi lake limaoneka lachimuna, anabadwira m’boma la Ntcheu ndipo pano akukhala mumzinda wa Blantyre ndipo amakhala ku hositelo ina pamodzi ndi atsikana omwe amasewera mpira wamiyendo.

Iyeyu anabadwa ndi chiwalo chachimuna chomwe akuti chili pamwamba komaso chachikazi chomwe wafotokoza kuti chili pansi pa chiwalo chachimunacho ndipo pamwamba pazonsezi, ali ndi mabere ngakhale kuti mawu ake ndi a mazenene ngati munthu wa bambo.

Akafuna kutaya madzi, Mphatso amagwiritsa ntchito chiwalo chachikazi komaso chopatsa chidwi kwambiri nchakuti munthuyu amakhalaso ndi nthawi ya msambo ngati momwe amapangira mzimayi wina aliyese.

Ali wa mng’ono, Mphatso adafusa mai ake kuti ndi chifukwa chiyani akuoneka wosiyana ndi amzake onse kumbali ya ziwalo, ndipo yankho lawo linali loti “mwanawe ndi mmene unabadwira, ife tinayesetsa koma zinakanika.”

Munthu yemwe akuti bambo ake sanawaone ndipo anangouzidwa kuti anapita ku South Africa ali wa khanda, anati ali wachichepele mai ake anamutengera kuchipatala cha Queen Elizabeth mumzinda wa Blantyre komwe ankafuna kuti akamudule chiwalo chachimunacho, koma akuti madotolo analephera.

Pa nthawiyo khololi mopanda chiyembekezo linavomeleza kuti ndimmene mwana wawo alili basi ndipo amangokhala kufikila pano pomwe Mphatso wabwera poyera ndikupempha thandizo kuti ngati mkotheka apite ku chipatala chakunja kuti akamudule chiwalo chimodzi ponena kuti akuvutika.

Chatsitsa dzaye mchakuti chiwalo chachimuna chikumamubweretsera chilako lako chofuna kugonana ndi mtsikana zomwe wati sangapange ndipo wati potsatira vutoli, posachedwapa anapitaso ku chipatala cha Queen Elizabeth yekha komwe anauza madotolo kuti amuthandize pavuto lakelo.

Ku chipatalaku, Mphatso anauzidwa kuti wachedwa kupitako kaamba koti pano ziwalozi zinakhwima ndipo chipatalachi chilibe kuthekera ndipo anamuuza kuti akuyenera kupita chipatala cha kunja kwa dziko lino kuti akathandizidwe.

Komatu munthuyu alibe kuthekera koti angakwanitse kupita kunja kukalandira thandizoli, mayi ake nawo sangakwanitseso kaamba koti pano nawo amachita kusungidwa ndi abale awo chifukwa cha mavuto azachuma, ndipo ichi ndi chifukwa chake Mphatso wapempha thandizo kwa akufuna kwabwino.

“Mmene ndakulamu ndaona kuti munthune ndili ndi vuto lomwe likukhudza moyo wanga kwambiri. Ndimathokoza amene ndikukhala nawo kuti tikamacheza amandichotsa nkhawa chifukwa pena ndikakhala ndekha ndimaganiza kuti kapena ndingodzipha chifukwa mwina pa dziko la pansi pano siine ofunikira.

“Ineyo kubwera kwanga ndikufuna kupempha kuti anthu andithandize. Ineyo ndilibe ndalama, sindingakwanitse, choncho anthu akufuna kwabwino andithandize ndipite ku chipatala akandichotse chiwalo cha chimuna. Ndikuvutika, ndi kusowa mtendere,” wadandaula Mphatso.

Ngakhale kuti chiwalo chachimuna pano chikumuzuza ndi chilakolako chofuna kugonana ndi mtsikana, Mphatso watsindika kuti mkati mwake amadzimva kuti ndiwa mkazi ndipo wati amavala zovala zachimuna kaamba koti maonekedwe a thupi lake amaoneka ngati mamuna ndipo wati poyamba ankavala zovala zachikazi koma amalandira zitozo zochuluka makamaka kwa anthu amene sakumudziwa zomwe zinapangitsa kuti asiye.

Koma ena mkumafusa kuti kodi Mphatso amati bwanji pa nkhani ya banja?

Munthuyu ngakhale kuti sanachitepo chibwezi kapena kugonana ndi mamuna kapena mkazi, wati banja amalifuna ndipo anati amafuna atadzakwatidwa ndi mamuna yemwe adzavomele chomwe iye ali.

Pakadali pano Lumbe wapempha anthu akufuna kwabwino kuti amuthandize wachisodzerayu kuti akadulidwe chiwalo chachimuna monga mwakuyankhula kwake ngakhale kuti pano pamasamba anchezo pabuka mtsutso kuti ndichiwalo chiti chomwe a za chipatala akuyenera kuchotsa.

Follow us on Twitter:

Advertisement

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.