M’busa wa mpingo wa Mvama CCAP mumzinda wa Lilongwe a Hamilton Yasin Gama abweretsa mtsutso pakati pa a Malawi pomwe anena kuti ana akazi omwe amahagana ndi bambo awo ndi opanda khalidwe.
Iwo amayankhula izi mumchiphuzitso chawo pamwambo wa mapemphero ammawa omwe anachitika lachinayi pa 5 January, 2023 ku tchalitchi chawo ku Lilongwe komwe anati zinthu zina zikuyenera kusintha pakati pa anthu okhulupilira zomwe ati zina sizili bwino.
A busa a Gama anati zinthu zina zomwe zikuchitika pano ngati sizingayankhulidwe, chikhilisitu chidzakhala chosaveka kuti ndi chiyani kwenikweni zomwe a kuti zizapangitsa kuti anthu amene sanamudziwe Yesu akanike kuvetsa potengera zochitikazo.
Apa anati anthu okhulupilira akuyenereka kukhala chitsazo chabwino pakati pa anthu ena ndicholinga choti amene sanatembenuke mtima akhale nako kukhutitsidwa ndikukhala ndi malingaliro ofuna kutembenuka mtima.
Mumchiphunzitsochi, m’busayu anati chimene chimamanga mudzi ndi khalidwe ndipo ati midzi yopanda khalidwe imapasuka kotelo kuti anthu akuyenera akhale ndi makhalidwe abwino zomwe akuti zimapititsaso patsogolo chikhilisitu.
Apa a Gama anati zinthu zambiri zikusokonekera kwambiri masiku ano kaamba koti makolo ambiri amakanika kupatsa ana awo mwambo kaamba koti nawoso makolowo sanalandire miyambo ya chikhalidwe kuchokera kwa makolo awo kalero.
Iwo anapeleka chitsanzo choti ana ambiri pano amadutsana ndi akuluakulu osapeleka ulemu komaso anati ana a kazi amahagana ndi bambo awo zomwe anati ndi mwikho komaso chizindikiro chakusowekera kwa khalidwe.
“Tili ndi m’badwo pano umene sukulandira chifukwa amayi awo amene awabeleka sanalandire. Ana tikukumana nawo pano ngati supatuka iweyo, nde kuti iwoso sapatuka. Ndi ana oti amahagana ndi a bambo awo, mabere awo kuombana ndi a bambo awo mpaka kukankha magalasi abambo awo, bambo awo mkukoza.
“Mavuto amene tikukumana nawo mmmakwalalamu tili nawoso mtchalitchi. Tili ndi akhilistu amene sanaleledwe, sanalandire ndipo sakudziwa kuti chikhilisitu ndi chiyani, alibe ndondomeko,” atelo abusa a Gama muchiphunzitso chawo.
Iwo anaonjezera kuti gwero la kusowekera khalidwe kwa ana ambiri ndi kaamba koti makolo ambiri akhalitsa sukulu zogonera komweko kuyambira ku sukulu zamkomba phala mpaka kukafika sukulu zaukachenjede kotelo kuti analibe nthawi yoti angalandire mwambo kuchokera kwa makolo awo zomwe a kuti zikupangitsa kuti ana ambiri akheloso opanda khalidwe pano.
Apa abusawa omwe anati anapatsidwa mwambo kuchokera kwa makolo awo, alangiza akhirisitu mdziko muno kuti aziphuzitsa ana awo makhalidwe abwino zomwe akuti zitha kuthandiza kuti m’badwo uno ukhale ndi anthu okhulupilira odziwa ndi kumvetsetsa chikhirisitu kuti ndi chiyani.
Pakadali pano pali kugawanika pakati pa anthu mmasamba anchezo pomwe mbali ina ikugwilizana ndi zomwe a Gama amaphunzitsazi pomwe ena atsutsa mwantu wa galu ponena kuti m’badwo wa pano kuhagana ndi makolo kumatengedwa ngati njira imodzi yoonetsera chikondi.
Mwezi wa February chaka chatha, a busa a Gama dzina lawo linali mkamwamkamwa kaamba kachiphunzitso chawo chomwe chinakwiitsa akuluakulu a gule wa mkulu pomwe mumchiphuzitso chawo china anati Mulungu amakonda aliyese ndipo amagwetsa mvula kwaochimwa kuphatikizapo anthu a gule wa mkulu.
Follow us on Twitter: