Pemphero Mphande wapempha omutsatira amuthandize kupemphera chifukwa mayi wina walota iye atamwalira

Advertisement

Wolemba Gracious Zinazi

M’modzi mwa anthu odziwika bwino pa tsamba la mchezo la Fesibuku wapempha anthu kuti amuthandize kupemphera chifukwa mayi wina walota iye atamwalira.

Mayiyu yemwe ndi wa zaka 42 ndipo sanazitchule dzina komanso komwe amakhala anafotokoza kuti iye walota kuti Mphande  amwalira pofika pa 22 April

“Ndinalota uli pa sitiletcha ku chipatala ndipo madotolo amathamangira nawe ku fiyeta, thupi lako linali magazi okhaokha, kenako ndinaziona ndekha ndikuwerenga nyuzipepala ya lachisanu pa 22 April ndipo munalembedwa Pemphero Mphande watisiya,” mayiyu wauza

Malingana ndi mayiyu, mu chaka cha 2011 analota mchemwali wake akulira kuti amuchotsa sukulu ndipo anakomoka ulendo unali omwewo. Patantha sabata atalota izi, zotsatira za kusukulu kwa mchemwali wakeyu zinaonetsadi kuti anachotsedwa.  Mchemwali wakeyo anasokonezeka maganizo, anadwala, kenako patantha miyezi iwiri anamwaliradi.

Chaka cha 2014 analota Peter Mutharika mtsogoleri, wakale wadziko lino, atanyamula baibulo akulumbira ndipo izi zinachitika, Mutharika anakhaladi mtsongoleri wadziko.

Kuonjezerapo, analotanso imfa ya mwamuna wake yemwe anamwalir pa ngozi ya galimoto ndimaloto ena omwe kumapeto kwake anachitikadi.

Mayiyu, kumapeto wanena kuti nkutheka malotowa abwera ndicholinga chopulumutsa moyo wa Pemphero kapena nkuthekanso akufuna kuti iye akonze zinthu zina zomwe zikufunika kukonzeka tsikuli lisanafike.

Poyankhapo, Mphande, kudzeranso patsamba la mchezo lake lomweli, wati chifukwa cha kulosera kwa malotowa, iye wati ali ndi mantha chifukwa chaka chanthanso wina anamulotanso atapanga mgwirizano wa miyezi itatu wa ndalama zokwana 17.8 million kwacha ndi kampani ina yaikulu, zotsatira zake izi zinachitika ndende.

Mphande wamaliza nkuthokonza omwe akuthandiza kupemphera komanso ena omwe akumulimbikitsa pomuimbira ma phone.

Iye wafotokonza kuti kuyambira mawa lolemba akhazikitsa mapemphero apadera ndi mtumiki wina wa Mulungu ndipo akhala akumaika pa tsamba lakeli ndondomeko yamapempherowa kuti onse ofuna kupemphera nao limodzi azikwanitsa kutsatira.

Advertisement