Osataya tsache lakale: Chakwera atuma Bakili Muluzi ku maliro

Advertisement

Yemwe adati chikuni chachikulu chimasunga moto adalinga ataona kaamba koti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera wasankha mtsogoleri wakale a Bakili Muluzi kukawaimilira ku maliro a mtsogoleri wakale wa dziko la Zambia a Rupiah Bwezani Banda.

A Banda omwe anali ndi zaka 85, amwalira Lachisanu sabata yatha pa 11 March ndipo thupi lawo likuyembekezeka kuikidwa m’manda Lachisanu lino pa 18 March kumalo omwe amaika atsogoleri adzikolo mumzinda wa Lusaka.

Ndipo malingana ndi kalata yomwe boma kudzera kuunduna owona zaubale ndimaiko akunja latulutsa Lachiwiri, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera asankha a Bakili Muluzi kuti ndi omwe akawaimilire kumaliloku.

Kusankhidwa kwa a Muluzi kukutsatira kutanganidwa kwa a Chakwera omwe lolemba sabata ino anyamuka kupita ku New York mdziko la America komwe kuli msonkhano wa maiko omwe akutukuka kumene pachuma.

Chikalatachi chati a Muluzi omwe amadziwikaso ndi dzina loti a Tcheya, akuyenera kunyamuka lachitatu kupita ku maliroko ndipo akuyenera kukakhala nawo pamwambo okhuza omwe uchitike Lachinayi pa Lusaka Showgrounds.

Poyankhapo pakusankhidwa kwawo, a Muluzi omwe akuyembekezeka kubwelera kuno kumudzi loweluka pa 19 March, ati zomwe achita a Chakwera kuwasankha iwowo kukawaimilira ku maliroku, ndiulemu waukulu.

Iwo ati anawadziwa a Rupiah Banda pomwe anali kukhala nduna yowona zaubale ndimaiko akunja.

Podziwa kuti mvula ikagwa kuchuluka zoliralira, kusankhidwa kwa a Muluzi kwadzetsa manong’onong’o pakati pa anthu mdziko muno makamaka mmasamba amchezo.

Anthu ena akuyamikira a Chakwera posankha a Muluzi ponena kuti mtsogoleri wakaleyu pokhala wamvula zakale sangakachititse manyazi dziko lino kumwambowu komaso anthu akuti a Muluzi ankadziwana bwino ndi malemu Banda.

Mbali inayi anthu akuti mtsogoleri wadziko linoyu amayenera kutuma wachiwiri wake a Saulos Chilima kapena imodzi mwa nduna zake osati a Muluzi.

Advertisement