A Mutharika akana kufunsidwa mafunso ndi ACB

Advertisement

Mtsogoleri wakale wadziko lino a Peter Mutharika akana kufunsidwa mafuso ndi bungwe lotsogolera ntchito yothana ndi katangale la Anti-Corruption Bureau (ACB) pankhani yakugwiritsidwa ntchito kwa nambala yawo ya TPIN pakugulidwa kwa simenti.

A Mutharika amayenera kufunsidwa mafuso ndi akuluakulu a bungwe la ACB lero Lachiwiri pa 27 July kudzera pa intaneti potsatila kulephereka kwa nkumano onga omwewu sabata yatha.

Koma kutatha nthawi yochepa kuti akuluakulu a ACB ayambe kufunsa a Mutharika, mtsogoleri opumayu anatulutsa chikalata chomwe amadziwitsa akuluakulu a ACB kuti iye sakufunaso kufusidwa mafuso pakugwiritsidwa ntchito kwa nambala yawo pakugulidwa kwa matumbaa simenti oposa 400 omwe analowa mdziko muno opanda kudulidwa msonkho.

Mumchikalatachi, chomwe tsamba lino lawona, a Mutharika awuza bungwe la ACB kuti lipeleke zifukwa zomveka zomwe likufunira kuwafusa mafuso pomwe iwo anafunsidwa kale ndi apolisi chaka chatha ndipo ananena kale kuti sakudziwapo kanthu pa zankhaniyi.

Iwo anati ndizokhumudwitsa kuti bungwe la ACB likufuna kuwafusa pa zankhaniyi pamene silikunena mlandu omwe mtsogoleri opumayu analakwa ndipo apa ati akuona kuti sipakuchitika chilungamo.

A Mutharika ati akana kufunsidwa ndi bungwe la ACB kaamba koti akuona kuti nkhaniyi yalowa ndale komaso ati bungweli likungofuna kuwazuza zomwe ati zitha kungowasokoneza kaganizidwe kawo ngati munthu.

“Ndizodabwitsa kwambiri kuti bungwe longa la ACB lomwe lili ndi ukadaulo pazofufuzafufuza litha kufuna kundifunsa mafuso opanda kundiuza mlandu omwe ndikuzengedwa.

“Poyang’anira zomwe ACB yakhala ikundipanga mmbuyomu, sizitheka kuti iwo andifunse mafuso, ndipo ndikuona kuti ndikuyenera ndiuzidwe mlandu omwe ndapalamula,” atelo a Mutharika.

Apa mtsogoleri opumayu watiso ngati bungwe la ACB likufuna kuwafunsa iwo mafuso pankhani yakugwiritsidwa ntchito kwa nambala yawo ya TPIN, ati bungweli likuyeneraso lifuse azitsogoleri onse opuma kuphatikiza achiwiri awo, osati iwo okha.

Advertisement