Pamene kusamvana kukupitilira pakati pa boma ndi bungwe loyimilira aphunzitsi la TUM, boma lakatenga chiletso ku bwalo la milandu kuti aphunzitsi abwerere ku ntchito.
Izi zikutsatira kunyanyala ntchito kwa aphunzitsi komwe kunayambiraso lachiwiri sabata ino kaamba koti boma likulephera kukwanilitsa pangano lake lomwe linanena kuti lipeleka ndalama kwa mphunzitsi aliyese yoti akagulire zozitetezera ku matenda a covid-19.
Nkhaniyi yakhala ikukanika kutha kwa miyezi ingapo tsopano ndipo lachinayi sabata ino akuluakulu aboma komaso TUM anakumana mumzinda wa Lilongwe komwe amakambirana zatsogolo la sitalaka ya aphunzitsiyi.
Koma zadziwika tsopano kuti pomwe mbali ziwirizi zinali m’chipinda chomata kukambirana za nkhaniyi, mbali inayi boma mwanseli linakagwadwa kubwalo la milandu kupempha kuti khothilo lilamule kuti sitalakayi yatha, aphunzitsi onse abweleleso ku ntchito.
Poyankhulapo za nkhaniyi, mtsogoleri wa bungwe la TUM a Willie Malimba ati ndizokhumudwitsa komaso zodabwitsa kuti boma lapanga chiganizochi pomwe kukambirana kunali mkati.
A Malimba ati apa zasonyezeratu kuti boma silikufuna kumva madandaulo omwe aphunzitsiwa akupeleka ponena kuti chodabwitsa kwambiri mchakuti zokambirana zilimkati, boma mbali inayi linazemba ndikupita ku khothi kukatenga chiletsochi.
“Ife ndife odabwa kwambiri ndiposo okhumudwa ndi zomwe lapanga bomali. Chodabwitsa kwambiri mchakuti izi zachitika pamene tinagwirizana ndi boma lomwelo kuti lachisanu lino tikhala tikumalizitsa zokambilana zathu zankhaniyi,” atelo a Malimba.
A Malimba ati zatelemu aphunzitsi akuyenera kupezeka kumalo awo ntchito lachisanu pa 9 April ndipo ati nkumano omwe umayeneleka kukhala pakati pa TUM ndi boma lero lachasanu, walephereka.
Pakadali pano bungwe la TUM silinabwere poyera kuti momwe zatelemu ilo lipanga chiyani potengera kuti zomwe akufuna zikuvuta vuta.