M’busa Mwai Kamuyambeni watuluka chipani cha DPP

Advertisement

Pomwe kukokanakokana kukupitililabe mu chipani cha Democratic Progressive Party (DPP), yemwe anali mkulu oyendetsa zinthu mchipanichi m’busa Mwai Kamuyambeni naye walembela kalata mlembi wamkulu za kusiya kwa udindo wake komanso kukhala membala wa chipanichi.

Abusawa mkalata yawo anayamba ndikuthokoza chipanichi powakhulupilila ndikuwapatsa danga lotumikira m’magawo osiyanaosiyana kuphatikizapo mkulu woyendetsa zinthu.

Iwo anapitiliza kuti aphunzira zambiri munthawiyi ndipo athokoza mtsogoleri wakale mwapadera.

A Kamuyambeni pomaliza anati ichi ndi chiyambi cha moyo wina ndipo akukhulupilira kuti azichezabe ndi anzawo omwe awasiya kuchipaniku.

Chipani cha DPP chakutidwa ndi mpungwepungwe kutsatira kugonja pa masankho achibweredza a pulezidenti omwe chidapambana ndi chipani cha Malawi Congress (MCP).

 

Advertisement