Kottana Maria Chidyaonga anachita kuphedwa

Advertisement
Malawi24.com

Dotolo oyeza mitembo m’dziko muno, a Charles Dzamalala, watsutsa zoti malemu Kottana Maria Chidyaonga adamwalira chifukwa chakulumidwa ndi njoka koma wati anadyetsedwa mankhwala.

Kottana wa zaka 23 adamwalira loweruka pa 4 January chaka chino.

Usiku wa pa 3 January, Kottana ndi mzake Diana Bhagwanji anali ku nyumba ya Timmy Mtilo komwe akuti analumidwa ndi njoka ndipo njokayo inaphedwa.

Awiriwa anamutengera mzawoyu kuchipatala cha Polyclinic atayamba kudandaula kuti amamva kuyabwa komaso amamva chizungulire ndipo kuchipatalaku ataona ndi momwe analili, anamutumiza ku Kamuzu Central komwe anamwalira atangofika.

Achibale a Kottana yemwe anali ndi zaka 23 anapempha katswiri popima mitembo, a Dzamalala, kuti apime thupi la m’bale wawoyo ndicholinga choti adziwe cheni cheni chomwe chidamupha ndipo apa ndipomwe zadziwika kuti malemuwa sanafe kaamba kolumidwa ndi njoka.

A Dzamalala omwe atulutsa zotsatira zakafufuku wawo pa imfa ya Kottana, atsutsa mwantu wagalu kuti malemuwa adafa kaamba kolumidwa ndi njoka.

Iwo ati malemuwa adamwalira kamba ka  mankhwala achiphe otchedwa tameki ndipo ati palibe umboni wa za sayasi kuti malemu wo adalumidwa ndi njoka.

“Imfayi siyachilengedwe ndipo yadza kaamba kakudya kapena kumwa chakudya/chakumwa chomwe munali mankhwala a chiphe otchedwa tameki omwe amapezeka m’misika yambiri mdziko muno,” watelo Dzamalala.

Chodzetsa tsembwe pankhaniyi mchoti katswiri oyeza mitemboyu wapeza kuti mtsikanayu sanamwe yekha tameki pofuna kudzipha kapena mwangozi ndipo ati pali munthu yemwe anamuchitila Kottana chipongwechi.

Advertisement