Mwikho: Bambo agwidwa akupanga zadama ndi galu

Advertisement
Police

Anthu m’mudzi mwa Chikandila mfumu yaikulu Mkanda m’boma la Mchinji alawulidwa pomwe mkulu wina anathawa mkazi wake kuchipinda ndikukagwidwa akuchita chisembwele ndi galu wake.

Watsimikiza zankhaniyi ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Inspector Kaitano Lubrino omwe azindikira mkuluyu ngati a Glandisoni Feliyala omwe ndi azaka makumi awiri (20).

Malingana ndi a Kaitano, a Feliyala anamangidwa pa 28 Disembala chaka chatha mkazi wawo atawapezelera buno buno bwamuswe alimchikondi ndigalu wapakhomo pawo.

Chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke mnyanga mchakuti, usiku wapa 27 Disembala, mkazi wa a Feliyala, anadabwa kuti bamboyu anakana atawauza kuti alowe mnyumba kuti onse akagone monga banja.

Apa mkaziyu mokhumudwa anangolowa m’nyumba nkukagona kuchipinda kusiya amunawo ali chete panja panyumba yawoyi ngati mlonda oyamba kumene ntchito.

Patatha pafupifupi ola limodzi nditheka, mkaziyu anadzidzimuka ndipo anadabwa kuti mamanuyo anali asanabwerebe kuchipindako kuzagona zomwe zinayamba kuwadetsa nkhawa.

Apa kaamba kachikondi komaso podziwa kuti chingaipe mchako, mai Jezale anaganiza zokawayang’ana amunawowo panja pomwe anawasiyapo ndipo anangoti kukamwa yasaa atawapezelera ali wefu wefu kugonana ndigalu wawo.

Mzimayiyu anathamanga kukauza anthu omwe anayandikana nawo nyumba kuti adzaonere limodzi malodzawo ndipo anthuwa atafika anapeza mkuluyu atanyamula galuyo ndikuthawitsana naye.

Tsiku lotsatila, mzimayiyu anatengera nkhaniyi ku polisi ya Chimwamkango ndipo apa apolisiwa anayamba kusaka mkuluyu ndipo anamumanga tsiku lomwelo mu dera lina komwe amabisala.

Atafusidwa cholinga chake pogonana ndigalu, Feliyala anati chinali chizimba Chomwe anauzidwa ndising’anga wina m’boma la Karonga komwe anapita kukatenga mankhwala olemeletsa ndipo zadziwika kuti aka sikanali koyomba kuchita izi.

Pakadali pano mkuluyu watsekulilidwa mulandu ogonana ndi nyama zomwe ndizotsutsana ndimalamulo oweruzira milandu gawo 153 (b) ndipo akuyembekezeka kukayankha mulanduwu posachedwapa.

Glandisoni Feliyala amachokera mmudzi mwa Malewa mfumu yaikulu Gumba m’boma la Mchinji