Sitikupanga nawo zionetsero – Asilamu

Advertisement
Dinala Chabulika

Anthu achipembedzo cha chisilamu m’dziko muno ati iwo satenga nawo mbali pazionetsero zomwe mabungwe omenyera ufulu akonza lachinayi lino.

Izi zikudza pomwe mabungwe omenyera ufulu mdziko muno akhale akupangitsa zionetsero zadziko lonse pomwe akukakamiza mkulu wa bungwe lazisankho la MEC a Jane Ansah kutula pansi udindo wake.

Amabungwewa omwe agwirana manja ndizipani zotsutsa ati mai Ansah analephera kuyendetsa bwino zisankho zapitazi choncho akufuna wapampandoyu kuti atule pansi udindo wake ndipo apempha anthu kuti akatenge nawo mbali pazionetserozi zomwe akuti zikhala zabata ndi mtendere.

Ngakhale izi zili choncho, anthu achipembedzo chachisilamu mdziko muno ati iwo satenga nawo gawo pazionetserozi.

Malingana ndi mneneri wa Muslim Association of Malawi (MAM) a Sheikh Dinala Chabulika, ndikwabwino kuti mabungwe ndi zipanizi apeze njira zabwino zothanirana ndinkhaniyi kusiyana ndikupanga zionetsero zomwe ati chipembedzo chawo sichimalora.

Sheikh Chabulika anati iwo sakuona chifukwa cheni cheni choti mpaka anthu akakamize wa pampando wa bungwe la zisankho la MEC kuti atule pansi udindo wake.

“Nthawi zonse ife timanena, mMalawi muno mukakhala ma demo timawauza asilamu onse ndipo timanenetsa kuti chisilamu sichimalora zimenezo chifukwa pachipembedzo chathu izi ndizolakwika.

“Kaya zili mu constitution koma ubwino wake sungakhale 100%. Njira yabwino ndikukhala pansi ndikukambilana ngati pali kusemphana. Ngati pali madandaulo njira yabwino ndiyopita nawo ku khothi ngati apangira azipaniwa,” watero sheikh Chabulika.

Pakadali pano, azitsogoleri azipani zotautsutsa za Malawi Congress (MCP) komaso United Transformation Movement (UTM) zamema otsatira ake kuti akatenge nawo mbali pa zionetserozi.

Advertisement

3 Comments

  1. Chabulika. kuzisaka that the not the position of muslim. Sell out

  2. Izi Akunenera asilamu akunyumba kwawo osati omwe tili mu Malawi Muno. Osamatiyika mawu mkamwa.

Comments are closed.