Gavanala wa chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP) mchigawo chakum’mwera Charles Mchacha wapempha mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) Lazarus Chakwera kuti asiye ndale ndikubwelera kutchalitchi.
Iwo amayankhula izi lamulungu pa bwalo la Mjamba mu mzinda wa Blantyre komwe chipanichi amasangalalira kuti chipanichi motsogozedwa ndi mtsogoleri wake a Peter Mutharika chapambana zisankho zapitazi.
Iwo anati ndizovetsa chisoni kuti chipani cha MCP chakhala chikudandaula zoberedwa chisankho kuyambira mchaka cha 1994 kufikira lero zomwe anati ndizosetheka.
A Mchacha anati kulephelaso kwa a Chakwera pazisankho za pa 21 May zikusonyeza kuti Mulungu sanasangalare kuti iwo anasiya nkhosa mumpingo wawo ndikuyamba ndale komaso ati izi zikusonyeza kuti izi anthu sanawakonde iwo.
Iwo anayelekeza a Chakwera ndi Yona wa m’bukhu lopatulika yemwe anakumana ndimavuto kaamba kothawa ntchito ya Mulungu pomwe anatumidwa kukalalikira mawu ake ndipo anati zomwe anachita Yona ndizomweso anapanga a Chakwera ndi chifukwa chake alepheraso zisankho zapitazi.
“Tinene lero pano kuti zimene akuchita pulezidenti wa chipani cha MCP mdziko muno polimbikitsa ziwawa, kulimbikitsa mtopola, sizimene Mulungu anamutuma iyayi. Mulungu anamutuma kukalalikira koma anasiya msewuwo ndikutenga chinthu chomwe sichili chake.
Ndipemphe pano mwaulemu kuti bwelerani mukalalikire Kutchalitchi, bwelerani mukapange mgonero, bwelerani anthu akusowa owabatiza. Mtsogoleri wabwino sangalimbikitse kuti mdziko muno mukhale mwazi iyayi.” Watelo Mchacha.
Iwo anapitiliza ndikunena kuti a Chakwera ndi atsankho kaamba koti akuthamangitsa anthu azigawo zina kuti asakhale pachigawo cha pakati mumzinda wa Lilongwe zomwe anati zikusonyeza kuti iwo sangakhale mtsogoleri wa dziko lino.
A Gavanalawa apemphaso azitsogoleri achipani cha MCP kuti ngati akufuna kuti chipanichi chiyende bwino, achotse pampando a Chakwera kaamba koti Mulungu akufuna kuti iwowa akamugwilire ntchito yake yolalikira.
Ukunena zoona mchacha chakwera abwerere Ku Church akalalikire
Zoona munthu wa Mulungu lero wasiya nkhosa zikuvutika kusowa mau a Mulungu akulimbana ndi ulemelero wa dziko lapansi za manyazi
Honourable Mchacha must not forget to tell the people who wrote MSCE for him???? He must not think that Malawians have forgotten or they don’t know about that scandal.