Inu muli ku DPP, ku UTM, ku UDF, ku Umodzi, ku Mbakuwaku ndi kwa a Kaliya a Sinodi ya CCAP ya Nkhoma akuti muwatsike lero mupite ku MCP komwe akutsogolera ndi a Chakwera.
Mu chikalata chimene mpingowu watulutsa lamulungu ndipo chinawelengedwa mu mipingo yake yonse, Sinodiyi yati pa zisankho za chaka chino a Malawi akuyenela kusankha munthu odzala ndi mzimu oyera komanso wa chilungamo ndinso oopa Mulungu.
Malinga ndi chikalatachi, a Malawi apemphedwa kuti asataye voti yawo povotela anthu amene ali mu boma pakali pano.
Ngakhal kuti Sinodi’yi sinatchule maina, iyo yanyogodola a Saulos Chilima a UTM ndi a Atupele Muluzi a UDF kuti iwo ndi anthu abodza chifukwa akulonjeza kusintha zinthu pamene akugwilabe ndi boma limene a Sinodi’wa akuona kuti lalephera ntchito yake.
Mwa zina a Sinodi anena kuti boma la DPP latchuka ndi mbiri za katangale komanso kusankhana mitundu.
Iwo potsogolera a Malawi ati anthu akuyenela kuzavotela mtsogoleri amene ali oopa Mulungu komanso odzala ndi mzimu oyela kudzanso osasekelela katangale.
Anthu ambiri atanthauzila kuti Sinodi ya Nkhoma ikumema anthu kuti avotele a Lazarus Chakwera a MCP amene poyamba anali membala wawo asanasiye ndi kukayamba ubusa ku mpingo wa Assemblies.
Koma ena atsutsa ndi kunena kuti pamene Sinodi ya Nkhoma yanena kuti munthu oyenela kusankhidwa akhale odana ndi nkhani za katangale ndiye kuti iwo achotsa a Chakwera mu nkhaniyi chifukwa iwo pano ali pa ubale wa ponda apa nane ndipondepo ndi Mayi Joyce Banda amene anthu amawaganizila kuti ndi munthu wa katangale ndi okonda zosolola.
Pa chisankho cha chaka chino anthu anayi ndiwo akuoneka kuti akuchititsana makani pa mpando wa u President. Awa ndi a Peter Mutharika a chipani cha DPP, a Lazarus Chakwera a chipani cha MCP, a Atupele Muluzi a chipani cha UDF ndi a Saulos Chilima a chipani cha UTM.
A Chilima ndi wachiwiri kwa a Mutharika pamene a Muluzi ndi nduna ya za umoyo mu boma la a Mutharika limene kalata ya nkhoma yanyoza mwa mphamvu.