Nkhuyu zodya a Malasa zapota a Chama

Advertisement

Akhirisitu a mpingo wa Anglican omwe sakukondwa ndi ulamulilo wa Bishop Brighton Malasa adaphwetsa galimoto za akiepisikopi Albert Chama yemwe anabwera kuti azakambilane ndi Akhirisituwa omwe sakuwafunaso a Malasa.

Akiepisikopi Chama omwe adali nawo pa msokhano wowunika nkhani yoti Bishop Malasa achotsedwe ku dayosezi ya Upper Shire adapempha mayendedwe agalimoto ina pomwe galimoto yawo inaphwesedwa matayala.

Akhirisitu sakuwafuna a Malasa

Nyimbo zosonyeza kusakondwa ndi a Malasa zidali pakamwa pomwe akuluakulu amakambilana ndi Akiepisikopi Chama.

Bishop Malasa akumuganizila kuti akusakaza chuma cha mpingo wa Anglican zomwe zakwiyitsa Akhirisitu ampingowu.

Ndipo Akiepisikopi Chama ati akhazikitsa kafukufuku pa nkhani yakusakazidwa kwa chuma cha mpingowu ndi Bishop Malasa.

Pakadali pano Akiepisikopi Chama wapempha Akhirisitu a mpingowu kuti adekhe pomwe nkhaniyi akuyifufuza.

Advertisement