Tisanamizanepo, ulendo wa CAF watha basi – watelo Osman

Advertisement
Yasin Osman

Ena mutha kumapusitsana, ena kumanena nkhaniyi mutafunda bulangete, awonso atha kumainena monong’ona kuti ena asamve. Koma mphunzitsi wa Noma wangomasuka ndi kuima pachulu kukamba nkhaniyi.

A Yasin Osman amene anatsogolera nyerere pa ulendo okakhomedwa ku DRC avomeleza kuti Noma singapitilile mu mpikisano wa CAF.

Yasin Osman
Yasin Osman: Noma singapitilile mu mpikisano wa CAF.

Polankhula atafika pa bwalo la Chileka, a Osman ananena kuti Vita ndi timu yaikulu ndipo Noma ndi ana kutalitali.

“Zonyengelelana tizisiye apo, Vita ija ndi a katundu. Zoti tingabwelele ndi zosatheka,” anatelo Osman.

Osman anaonjezelapo kunena kuti cha nzeru chomwe angachite Manoma ndi choyesetsa kuti age ndi ulemu.

“Akabwela, ofunika tizapambane koma zoti tingamwetse zigoli zisanu ine ndiye sindikuona zitatheka,” Osman anatelo.

Koma Joseph Kamwendo amene ndi Mtsogoleri wa osewela a Noma watsutsana ndi Osman.

“Ndi zotheka kuifafantha Vita ija, bola kuikapo mtima basi,” anatelo Kamwendo.

Noma inakunthidwa ndi zigoli zinayi kwa du ku DRC. Kuti ipitilire ikuyenela kuchinya zigoli zisanu kwa du pa Bingu National Stadium.