Tisanamizanepo, ulendo wa CAF watha basi – watelo Osman

Advertisement
Yasin Osman

Ena mutha kumapusitsana, ena kumanena nkhaniyi mutafunda bulangete, awonso atha kumainena monong’ona kuti ena asamve. Koma mphunzitsi wa Noma wangomasuka ndi kuima pachulu kukamba nkhaniyi.

A Yasin Osman amene anatsogolera nyerere pa ulendo okakhomedwa ku DRC avomeleza kuti Noma singapitilile mu mpikisano wa CAF.

Yasin Osman
Yasin Osman: Noma singapitilile mu mpikisano wa CAF.

Polankhula atafika pa bwalo la Chileka, a Osman ananena kuti Vita ndi timu yaikulu ndipo Noma ndi ana kutalitali.

“Zonyengelelana tizisiye apo, Vita ija ndi a katundu. Zoti tingabwelele ndi zosatheka,” anatelo Osman.

Osman anaonjezelapo kunena kuti cha nzeru chomwe angachite Manoma ndi choyesetsa kuti age ndi ulemu.

“Akabwela, ofunika tizapambane koma zoti tingamwetse zigoli zisanu ine ndiye sindikuona zitatheka,” Osman anatelo.

Koma Joseph Kamwendo amene ndi Mtsogoleri wa osewela a Noma watsutsana ndi Osman.

“Ndi zotheka kuifafantha Vita ija, bola kuikapo mtima basi,” anatelo Kamwendo.

Noma inakunthidwa ndi zigoli zinayi kwa du ku DRC. Kuti ipitilire ikuyenela kuchinya zigoli zisanu kwa du pa Bingu National Stadium.

Advertisement

49 Comments

  1. Ngat coach wanena ndiye kut bas palibe chabwno pot masapota anoma makani ngat ofula agaku kaya zanu izo muziona

  2. It wz obvious kutero cz AS Vita ili ndi ma proffessional players en mind yu even pa Africa pano ili ndi mbiri ndie u a busy talking shit kt bola Bullets, as long as Fifa z concerned Bullets z jst nothing pa nkhani ya mpira.Mpira kwathu kuno kulibe tiyeni tizivomereza mxieeeeeeeee!

  3. abwana ndinu abodza kwambiri…Coach amene mukumunenayo walankhula kuti chilichonse ndichotheka mumpila komanso ndicoach uti amene anganene zopusa ngati zimenezi pamene kuli masewera ena oti amenyedwe???.iweyo paja tinakudziwakale kuti ndiwe Wabullets ndipo anthu ambiri chidwi chawo chotsata nkhani zamasewero kudzela pa tsambalino(malawi24) likuchoka chifukwa chainu amene mumaonetsa mbali polemba nkhani zamaseweo.chonde chonde sinthani malume….

  4. Ine pheee kudikila mtibu wina wazgoli dis coming mid week! kkkkkk vita singabwelere kuzagawa tiger love.

  5. chilungamo chimawawa! koch wanena ngamo si nanga vita adaiona ndi maso ake,Ndie vita izangoonjezera 4 kwa iyayi,mu aggregate vita 8,noma 0.

  6. Team yathu ili bwino taikwapula Bullets 2 kwa duuu ,eeeee Joseph kamwendo ndi machine anakabwerako ndi ntibu wa dzigoli

  7. ndye kut tisazivute ndkupta pa Bingu kukaonera masewero achibwereza hahahahahah kom #Osman akufuna kuchotsedwa ntchto et

  8. Noma ilibe coach yasin osman kunena mosanamizana satha coaching …ma players tilinawo abwino koma luso la coaching tilibe …..even superleague ikanatikanika becouse of poor tactics from yasin osman just imagine the system he used at Vita, making things worse he dropped kaliati and chade becouse of his system…wadabwa is too heavy to cope up with as vita’s pace, chande and kaliati would have tried.

    he is now talking nosense that also shows that he is not a leader, in football we dont talk like that becouse anything can happen…. Noma tiyeni timuchitise manyazi osman poyiphula game and after the game he should be fired.

Comments are closed.