Iphani owotcha makala – Winiko

Advertisement
Charcoal Malawi

Mmutu mwa phungu wa Kum’mwera kwa boma la Mulanje a Bon Kalindo otchuka kuti Winiko muli chilango chimodzi basi pa mlandu ulionse, kupha basi.

Patapita nthawi a Kalindo atapempha boma kuti lizipha anthu onse okupha anthu a khungu la chi albino, pano a Kalindo aona anthu ena oyenela kuphedwa. Amenewa ndi owotcha makala.

Bon Kalindo
Bon Kalindo: Apheni basi mukawapeza.

Malinga ndi a Kalindo, anthu onse opezeka akuotcha makala akuyenela kuphedwa, chandamale ya pompo pompo.

“Anthu amenewa akuononga dziko lino, angodula mitengo ndi kumabweletsa mavuto osiyanasiyana. Apheni basi mukawapeza,” anatelo a Kalindo.

Iwo ananena izi mu nyumba ya malamulo ku mayambililo a sabata lino.

Koma a bungwe la Forum for National Development adzudzula kolimba a Kalindo. Iwo ati a Kalindo aziyankhula ngati m’dindo. “A Kalindo ndi phungu, akuyenela kudziwa kuti anthu ngakhale olakwila malamulo ali ndi ufulu,” anatelo a Flyson Chodzi a bungweli.