Zayambika ndale: nkhalakale zilowa DPP

Advertisement
Democratic Progressive Party

2019 sali pafupi kwenikweni koma ndale zija ndiye zafikapo basi.

Pamene chipani chotsutsa cha Kongeresi chili pa kalikiliki otolela anthu, nawo a chipani cholamula cha DPP ayambapo kutsegula makomo awo.

Dzulo lamulungu chipani cholamulachi chalandila njonda zinayi zomwe ndi nkhalakale pa ndale.

Democratic Progressive Party
Chipani cha DPP chalandila njonda zinayi.

Pa msonkhano omwe anachititsa a Peter Mutharika ku Lunzu mu boma la Blantyre, chipani cholamulachi chatola anthu anayi omwe agawanitsa maganizo pakati pa a Malawi.

A DPP alandila Bambo Henry Phoya, a Brown Mpinganjira, a Ken Lipenga kudzanso abusa a Daniel Gunya.

A Phoya ndi a Lipenga anakhalapo mu chipani cha DPP ndipo anagwilapo ngati nduna ndi President Bingu wa Mutharika amene anayambitsa chipanichi. Awiriwa anasiya chipanichi atamwalira a Mutharika. Iwo kenako analowa PP ya a Joyce Banda. Pa zisankho za 2014, anagwa chagada.

A Mpinganjira akhalapo nduna ndi boma la a Bakili Muluzi, pa masankho a 2009 iwo anaima ndi a John Tembo a MCP ngati achiwiri awo. Analowa mu chipani cha PP chitayambitsidwa ndi Mayi Banda.

M’busa Gunya anadziwika kwambiri pa nthawi imene a Muluzi amafuna kuimila kachitatu angakhale kuti malamulo samawalola. A Gunya adatsogolela bungwe la PAC kukana zofuna a Muluzi.

Akatswiri pa ndale asiyana maganizo pa nkhani ya anayiwa kulowa mu DPP.

Pamene ena ati chipani cha DPP chiphukila, ena ati anthuwa alibe ntchito kwenikweni.