Zayambika ndale: nkhalakale zilowa DPP

Democratic Progressive Party

2019 sali pafupi kwenikweni koma ndale zija ndiye zafikapo basi.

Pamene chipani chotsutsa cha Kongeresi chili pa kalikiliki otolela anthu, nawo a chipani cholamula cha DPP ayambapo kutsegula makomo awo.

Dzulo lamulungu chipani cholamulachi chalandila njonda zinayi zomwe ndi nkhalakale pa ndale.

Democratic Progressive Party
Chipani cha DPP chalandila njonda zinayi.

Pa msonkhano omwe anachititsa a Peter Mutharika ku Lunzu mu boma la Blantyre, chipani cholamulachi chatola anthu anayi omwe agawanitsa maganizo pakati pa a Malawi.

A DPP alandila Bambo Henry Phoya, a Brown Mpinganjira, a Ken Lipenga kudzanso abusa a Daniel Gunya.

A Phoya ndi a Lipenga anakhalapo mu chipani cha DPP ndipo anagwilapo ngati nduna ndi President Bingu wa Mutharika amene anayambitsa chipanichi. Awiriwa anasiya chipanichi atamwalira a Mutharika. Iwo kenako analowa PP ya a Joyce Banda. Pa zisankho za 2014, anagwa chagada.

A Mpinganjira akhalapo nduna ndi boma la a Bakili Muluzi, pa masankho a 2009 iwo anaima ndi a John Tembo a MCP ngati achiwiri awo. Analowa mu chipani cha PP chitayambitsidwa ndi Mayi Banda.

M’busa Gunya anadziwika kwambiri pa nthawi imene a Muluzi amafuna kuimila kachitatu angakhale kuti malamulo samawalola. A Gunya adatsogolela bungwe la PAC kukana zofuna a Muluzi.

Akatswiri pa ndale asiyana maganizo pa nkhani ya anayiwa kulowa mu DPP.

Pamene ena ati chipani cha DPP chiphukila, ena ati anthuwa alibe ntchito kwenikweni.

 

Advertisement

54 Comments

 1. Zitsiru zizkavotera nkhalamba z opanda ntchito, kodi pa malawi tilibe angayendese n dale koma mbavazi basi . Anyamata oti angayendese dziko ngati a Chilima, Kaliwo, Atupele , Chihana ku malawi kuno kulibe? Kukacha basi tizingomva za anthu ozungulira mituwa, since 1994

 2. KUGANIZA MWAKUYA DPP IKUPITA BASI ZITUKUKO MUKUZIONA NOKHA AMENE SAKUONA NDI TOMASI DIDIMU MWASALA ENANU BWERANI IFE PAKA TILAMULIRA PAKA WOOH MUMANGOLALATA GAIWA WASHIPAU ATHU OPANDA ZERU ZISIRU AGARU ANAKALIZI ATHU ODYA ZOTOLA INU MULIBE OLO NDIKATHU CHAKWERA AKAZAWINA MU

 3. Pa anthu amene arowa chipani cha DPP paribe amene angapikisane ndi sidik mia ,pamenepo msaganize kuti mwawonjezera mavote ambiri ayi ndi atatu omwewo basi

 4. Hahahaha this is terrorists politicians ..mcp don’t afraid of this four guyz proceed your journey and we will see akuchokanso kumeneko mukudziwabwino za Mpinganjira prostitute politician ndiye ameneyu

  1. Zako #Phulika, Padzana #Anong’a, Munawaombela Mmanja After 48 Hrz Ndikuzakusasani, Munayamba Kunyoza Gat Mukunyozela Anthuwa, Muli Ndi Problem Anyau

 5. Inu amene afuna atha kulowa kapena ayi Dpp,koma palibe omwe ndikuwaona kuti angachose Dpp.mkuona pali kusiyana pakati pa by/general election,ndiye poti mcp ikuona ngati izawina chifukwa cha by-election Muzaziona.

 6. inu a mcp mmafuna ajoine chipani chanu? ndima political prostitutes inde koma ndiozindikira aonamo tsogolo muulamuliro wa Peter ndichifukwa ajoina DPP
  chikakhala chipani cha lazaro chanucho nchatsogolo ithink akanaku joinani hahaha shame on you
  mungochedwapo chabe mukamalimbana ndi DPP
  kasewereni kutali

  1. Iwe #kaombe, Mia Anayamba Ku Udf, Dpp Anatuluka Maliro Bingu Atangolegeza Kumene Ndikupa Pp Kumeneko Ananyanyala Kt Sanasakhe Udindo Gat Akuufa Ku Chipan Chanu Cha Ang’ona Pano Ali Kwa Ang’ona, Nde Zikusiyana Bwa?? Kkkk

 7. Enawa anolowa kale DPP, why propaganda is it not the same Ken Lipenga who joined DPP last year and now again has joined again kkkk , tikukuonani

 8. Inu aMW24 zanu zimenezo ife tikungoti welcome our political prostitutes.kkkkkkk olo m’banja mmene umakhala ndi ana ena omwe ndi mahule koma sumawataya amakhala wana akobe baasi! so awawa ndi Anthu baasi 1s again wlcm apse mtima ndi Wa #Chakwera zake zimenezo kkkkkkk.

Comments are closed.