Zilibe ndalama nyerere: miyezi yatha tsopano osalipila ma Kochi

Advertisement
Super League Malawi

Apambana ligi, kawiri konse kufika mu ndime yotsiliza ya mipikisano ndipo akukamba zopita ku mpikisano wa CAF koma manoma ali ndi mthumba moyela.Maluzi ngati khoswe wa mu kachisi.

Super League Malawi
Osman: Ndalama zathu sakutipatsa mwezi ukatha.

Malinga ndi malipoti, akatswiri a ligi chaka chino a nyerere ati akulephela kulipila aphunzitsi a timuyi ngakhale kuti apambana ligi komanso akukhalila chithumba cha ndalama cha kampani ya ku Japan ya Be Forward.

Malipoti amene anatsindikidwa mu nyuzipepa anaulula kuti aphunzitsi a noma akhala asakulandila chawo cha pa mwezi kuchokela mu mwezi wa August.

Mphunzitsi wamkulu ku noma, a Yasin Osman anatsimikiza kuti chioneleni malipiro awo mwezi wa August, kwinaku angokhala kamba kokonda timu.

“Pano sitikudziwa kuti nkumakhala bwanji koma za ndalama izi ndiye ah sakutipatsa zathu mwezi ukatha,” anatelo a Osman pouza olemba nkhani.

Ndipo akuluakulu a timuyi nawo anatsimikiza kuti kuli maluzi ku Lali Lubani kumene amene akuwakanikitsa kulipila aphunzitsi awo.

“Koma tikulongosola zimenezo. Inu mtima m’malo. Pompano ayimba lokoma aphunzitsi amenewa,” anatelo wapampando wa nyerere a Gift Mkandawire.

“Anthu amvetse kuti chithandizo chochoka ku Be Forward chimapita ku malipiro a osewera basi, aphunzitsi siziwakhudza ndiye timayenela kulongosola zimenezo tokha,” anatelo a Mkandawire.

Iwo anaonjezelapo kuti Mmbuyomu nyerere zakhala zikudalila anthu akufuna kwabwino ndi kangachepe kotola ku masewelo kuti alipile aphunzitsi awo.

“Ndiye pakati apa masewelo athu anali ndi ana basi, osatibweletsela phindu lenileni,” a Mkandawire anamaliza choncho.