Ife tikuti kunsewu toto – atero ophunzira

Advertisement
poly-unima-university

Ophunzira msukulu zaukachenjede mdziko muno atemesa nkhwangwa pamwala kuti sapita nawo ku msewu kukachita zionetsero sabata lamawa.

Bungwe loyang’anira zipembedzo mdziko muno la Public Affairs Committee (PAC) lamema anthu kukachita zionetsero lachitatu likudzali pofuna kukakamiza boma kuti likonzeso malamulo oyendetsera zisankho mdziko muno.

Chanco students
Ophunzira msukulu za ukachenjede ati satenga nawo mbali pa zionetserozi.(File)

Mipingo yambiri yaonetsa chidwi chokapezeka kuzionetserozo zomwe malingana ndi bungwe la PAC zidzakhala za mtendere ndipo mipingo monga Anglican komanso Katolika kungotchula yochepa yamema oyitsatira kuti azatenge nawo mbali pazionetserozi.

Fisi anakanadi msatsi; Ophunzira msukulu za ukachenjede za Chancellor College komaso Polytechnic omwe ndimasukulu amene amadziwika bwino ndikupanga zionetsero ati iwo satenga nawo mbali pa zionetserozi.

Izi ndimalingana ndichikalata chomwe ophuzila msukuluzi atulutsa chomwe otikitila wake anali mlembi wagulu lina lomwe likutchedwa ophunzira okhudzidwa, a Chrispin Mahara.

Gulu la ophunzira okhudzidwali lati iwo ngati achinyamata okonda dziko la Malawi komanso odzipereka pa chitukuko cha dziko lino, asankha kusakhala chete koma kuyankhulapo pa nkhani zimene zamanga nthenje m’dziko muno makamaka pa zionetsero zimene zakonzedwa ndi PAC.

Iwo ati ngati achinyamata, ali okhudzika ndipempho loti akayende nawo pamsewu pa 13 disembala, pofuna kukakamiza boma kuti likonzenso malamulo oyendetsera zisankho m’dziko muno.

“Ife sitikutsutsana ndi ganizoli, koma ngati a Malawi komanso achinyamata omwe tili odzipereka kumpingo tili ndi mantha ngati nkhosa zokaphedwa pazifukwa izi: Sitinaiwale imfa yomvetsa chisoni ya a Malawi anzathu 19 amene anaphedwa, 58 amene anaombeledwa ndi ena ochuluka amene anavulazidwa modetsa nkhawa chifukwa cha zionetsero zonga zoterezi pa 20 Julaye, 2011.

“Tikudziwa kuti iwo ngati azitsogoleri mwina amvetsetsa kuti malamulo akufunikawo ndiotani ndipo ubwino wake ndi otani, koma adziwe kuti anthu ochuluka sakudziwa bwino za malamulowa. Kodi a Malawi ndi owapindulira motani? Pa chifukwa ichi nzotheka kuti pazifukwa zokomera iwo okha akufuna anthu aluze miyoyo, akatundu ndi tsogolo pa mfundo zimene mwina a Malawi ena alibe nazo vuto,” latelo gawo lina la kalatayo.

Ophunzirawa alangizaso a Malawi kuti asalore kuti kukhulupirika ndi kudzipereka kwawo ku mipingo yawo yosiyana kutengeredwe pa mgong’o.

Iwo ati ngati achinyamata amene anadalilidwa kuti apitilize maphunziro a ntchito zosiyanasiyana akupempha a PAC apeze njira ina yabwino koma zowatengera ku msewu ayi.

“Mzako amadutsa apa wagwa ndipo watchola mkono, wa nzeru podutsa amalambalara m’mbalimo. Pa 20 Julaye 2011, zoopsya tinaziona, mizimu ya anyamata anzathu ikukumbutseni china chake. Ife tasankha kulambalara m’mbalimo, tikuti kumsewu toto,” atelo ophunzira okhudzidwawa.