Sizinayende manoma ku Karonga: wamkulu waonetsedwa mbwadza

Advertisement

Mawa ndiye kuli Moyale ija inawagweba ndi kuwapilikitsa mu chikho cha FISD.

Manoma zawavutanso.

Lero ndiye Chitipa ndi iyi yaliza nyerere.

Sizili bwino ku manoma pamene lero alephela kuikamo olo chimodzi chenicheni pa masewelo amene amakumana ndi timu yomwe ili pansi penipeni pa ligi ya Chitipa United.

Pa masewelo amene anachitikila pa bwalo la Karonga limene alitsegula kumene, manoma akhumudwitsa owatsatila atasowa mwayi obooleza kuti atolele ma pointi atatu.

Zimaoneka ngati nyerere sizivutika potengela kuti Chitipa ili pansi penipeni pa ligi ndipo ulendo wawo otuluka ukukhala ngati ndi okonza kale.

Koma nyerere ayi ndithu zinakanika kuluma ndi kumangochinya pambali kapena pa mwamba kupitiliza kupsetsa mtima owakonda.

Anyamata a nyerere amene akhala akuonetsa mbwadza anzawo akuoneka kuti lero analibe ukali.

Mawa lamulungu, nyerere zikhala zikuphana maso ndi maso ndi Moyale imene inawakhoma mu chikho cha FISD.

Advertisement

150 Comments

 1. Anthu aku chitipa chimene amadziwa ndi Ku khwima vuto palibe zinayambira kwa ng’ono wathu pa Mzuzu stadium bolani anthu athuwo abwera bwino moti ndikunena pano abwerera Ku BT ndi 4 points atayimenya Moyale pa HOME

 2. Adm Khalani ozisata 0_0 ndikuona mbwaza ngati inalowa mu super lg imeneyo ndiyayikuluso so thats beta result we are moving forward noma 4life

 3. Kodi aganyu mukadachulukirabe koma ganyu yanuyo izakuphetsani kupanga drow ndiye chifukwa mutawonere lero tikunkhazulani muwona mawule wamkamka basi a bb pano angonjenjemera ngati mavu pa chisa chake kuti akumaneso ndi akulu akuluso

 4. Admin achoke saonetsa mbali pa group ngati ukufuna udzimuthandiza danger pa times muchuruke ansanje& noma bwanji

 5. mapazi ake azikang’a ameneyo always Noma osamakamba za Embassy fc bwanji? silver yapanga draw ndi blantyre united koma sukukamba kathu koma always Noma why?

  1. Nkhani sikutimvetsa kuwawa mayazi nkhani ndiyakuti inuyo mukamapita koyenda kaya muli pa home mumatokota kwambili ndizomwe zikupangitsa kuti anthu akutsatileni ndi mulomo wanuwo.Pajatu amati ukayenda siya phazi ukasiya mulomo udzakutsa.

  2. Taonera Ena Amvera Mpira Wa Athakati. Ena Nkumat Ngongoliwa Fc Ena Akuti Ayi Koma Akhale Namapopa Fc Poti Zonse Nzamasenga.

 6. Munathamau Bullets itadrawetsa ngat inuyo mumadoda kuposa bullets. muonanso lero ndimoyale aphwathuuuuu…saizi yayamba kuthina pang’onopang’ono ndipo simunat ithinad zenizeni mpaka mutayambiranso kumakodzera pagolo mwina.

 7. I can see admin wa pano z against noma ndithu…zolemba zakuthera sungamakambeko nkhani zina koma uzingokamba za noma bas?? Shame on u ndithu noma stl on position udziluma ku msana kwako komwe tsopano

 8. ndiye ganyu ameneyu wakuva neba ubwebweta zenizeni mawa tikutenga 3points ndie neba minibus yakoyo ikugwa kudzenje iyo mabwebweta uziona chaka chake ndichino ndie usaiwale neba mulandu uja waliripila ?

 9. Koma galu imeneyi. Tiona mawa tikawina kuti udzanena chani. Poti ndiwe galu umayiwala msanga eti.Moyale tayichinya kangati ife.Kulibe timu ingasewere ma game anayi muma ola ochita kuwerengeka.Ngakhale ku England kumene Conte ndiyomwe amadandaula atasewera champions league tuesday kenaka saturday ndikukumana ndi City.Ngati umautsata mpira galu iwe ukudziwa zimwe Conte amadandaula. Nanga kulibwanji kusewera ma game anayi mosatidzana.Ubwino wake tiludze kaya kuwina sitiyendera zamaganizo ako nyani iwe wamva.Tidzakondabe Manoma mbuzi iwe wamva

 10. MADRID – Barcelona will offer Lionel Messi a lifetime contract at the club, CEO Oscar Grau said on Saturday.

  Messi, 30, agreed a four-year deal with Barcelona in July, although has not officially signed it yet.

  Grau, speaking at the club’s annual general meeting, said the Argentine forward would be offered a similar deal to the one Barca’s Spanish midfielder Andres Iniesta signed this month.

 11. Admin iwe ndiye wanama ngat ife anoma taona mbwaza bwanji tidakali pa chiongolero mu ligimo 51 points zimenezo iwe sukuziziwa

 12. Chokani apa mwazolowela zomamwana magazi basi ku Karonga nakoso ndi chimodzimodzi. Mwaluza vomelezani kuti ana akukunthani asa, kukhalira minyozo basi Voetsek zano

 13. nothing strange coz samatha mpira ndipo league sangatenge moti abwelerako ndi 1 point kumpotoko ngati DPP kupeza 1 kkkkkkkkkk noma sizampira mumangodziwa kupelekeza yotenga ndi BB zikavutitsitsa Silver winawe iwalako

  1. wachepa aixe ine ndiye ozitsatayo mmesa mumkatiseka titadrawer ndi chitipa kenako mkuluza ndi moyale inuso mudutsa momo mubwelera ndi 1 point

 14. Chokani APA asaaah! ni team wuli yambula kwendela juju pala yikusewera bola??

  Use whatever you can afford in order to get the results.

  wakambwe imwe!!!!

 15. Drama pa Karonga Stadium. Zinayamba mateam akuchokera kopumira. Ma official a Chitipa amayenda ndi kamwana ka zaka 12 kuchokera ku dressing room. Chodabwisa chinali choti mwanayu amamupasa ulemmu komanso chitetezo chachikulu. Izi zinadabwisa achina Yona Malunga, butao ndi mabaunsa ena a noma omwe anafunitsitsa kuti mwanayu asatuluke ku dressing room. Anafunisisa kukamenya kamwanaka koma zinatengera apolisi about 12kukapulumusa kamwanaka. Bata linabwerera. Chamma 60 minutes, mpira unatuluka pafupi ndi mzere wapakati, panthawiyo nkut golly wa Cp utd anavulala. Ted sumani anasekesa anthu atatola mpira nkuthamanga nawo mmanja ngat rugby kukauponya mu net ya Cp utd. Abel mwakirama ataona izi anautola mpira uja nkuthamanga nao kukapanga chimodzmodz pagolo la noma. Apa nkut ref ali busy ndi golly wa Cp utd.. Chinanso nchoti Chipuwa anadabwisa anthu pomwe amakakamira mpira umodz wokha pa mipira 8 yomwe imagwiritsidwa ncthito. Bolera akamupatsa mipira inayo iye amaikana mpaka wakewo ubwere. Ref anampatsa yellow pachifukwachi.. Ndathira pano *_Lenokisi_*

  1. chule iwe,anatenga mpira ndi player wachitipa ngat nkhan simukuyidziwa kumangokhala chete,,,mpira unali live pa zodiak nde ngat wakhuta kwambiri kuli bwino kugona stop using your unus wen spkng

Comments are closed.