Amunjata chifukwa chonama za ‘anamapopa’

Advertisement
Mangochi

Inu amene mukumadzuka usiku ndi kumakolezera moto pa nkhani zopopa magazi, samalani chifukwa Apolisi ayamba kunjata anthu a mkhalidwe onunkhawu.

Mkulu wina wa mu boma la Zomba walamulidwa kukakhala ku ndende kwa miyezi itatu chifukwa chonama kuti kuli anthu opopa magazi.

CourtMalinga ndi Apolisi, a Bambo Stanford Bamusi a zaka 49 anadzuka pakati pa usiku pa 16 Okotobala ndikuyamba kukuwa kuti mmudzi mwawo mwabwela opopa magazi.

Anthu adathawa m’nyumba mwawo ndi kukagona kutchire ati poopa kupopedwa magazi ngakhale kuti mderalo munalibe zimenezo.

Apolisi atamva izi, adamunjata mkuluyo ndi kumutsekela mu chitolokosi.

Atapita naye ku bwalo, iye anapezeka olakwa pa mlandu ofuna kudzetsa chisokonezo ndipo walamulidwa kukhala ku ndende kwa miyezi itatu.

Ngakhale mlandu otele munthu amaloledwa kupeleka chindapusa, bwalo linakana.