Dalaiva, kondakita amangidwa chifukwa chonyamula ma 4 – 4

Advertisement
cuffs

Ku Phalombe, Dalaiva wina wa minibus ndi kondakita wake atsekeledwa mu chitolokosi kamba konyamula anthu ngati matumba a mbatata.

Apolisi mu bomalo ati atsekela awiriwo kamba koti ananyamula anthu makumi awiri kudza mphambu zinayi (24) mu minibus imene inapangidwa kuti izinyamula anthu khumi ndi asanu ndi mphambu imodzi (16).

“Ananyamula ma folo folo pampando, kuwapanga anthu ngati matumba. Anayika moyo wa anthu pa chiopsezo,” anatelo Apolisi.

Awiri atsekeledwawo ndi a Steven Lawrence a zaka 34 ndi a James Bwanaisa a zaka 29. Iwo anali mu minibus ya  Nissan Caravan.

Aka ndi koyamba kuti Apolisi mu boma la Phalombe amange anthu kamba koswa malamulo a pamseu.