
Mfumu Zatuwa ya m’boma la Kasungu yanjatidwa ndi a Polisi chifukwa choganiziridwa kuti yagwilirira mnzimayi wamisala m’munda wina wa chimanga muderalo.
Malinga ndi m’neneri wa Polisi ku Kasungu Joseph Kachikho, mfumuyi inachita zoospazi m’mudzi mwa Kadongo m’dera la Mfumu yayikulu Chisanga m’bomalo.
Kachikho wati pakhala pali malipoti kudelaro kuti mfumuyi yomwe dzina lake ndi Yohane Nyirenda ikumapakula mopanda chisoni mnzimayi wamisalayu, ndipo la 40 linamukwanira.
Pa tsiku lomwe mfumuyi inagwidwa, m’chimwene wa mayi wamisalayu, Rodwell Nyirenda anapeza mfumuyi m’munda wa chimanga itapanilira mnzimayiyu kukhuthula zilakolako zake zosakhala bwino, ndipo mayi wamisalayu anathawa kuyisiya mfumuyi ili chibadwire mfuti idakali ndi moto wonse.
Mfumu yosazigwilayi, yoyenda mkabudula muli njo ikawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kukayakha mlanduwu.