A bungwe anangotinyenga – atelo ophunzira a ku Chanco

Advertisement
Chanco

Ophunzira a ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor ati bungwe loona za ufulu la HRCC linangowanyenga basi.

Ophunzira a ku sukuluyi anena izi patatha chaka bungwe lomenyela ufulu ili litalonjeza kuti lifufuza nkhanza za Apolisi zomwe anachitila asungwana a pa sukuluyi.

Pa zionetselo za chaka chatha zomwe ophunzira pa sukuluyi adachita pofuna kuti ndalama zomwe amalipila zitsike, Apolisi anajambulidwa akuswa makofi atsikana awiri a pa sukulupo.

Zitachitika izo, a bungwe la HRCC analonjeza kuti afufuza nkhaniyi koma kufika lero ati kuli chete.

“Kukhala ngati zinali ntchetela zoti afufuza zija chifukwa kufika lero kuli ziii. Anatipaka phula m’maso basi amene aja,” anatelo a Ayuba James amene ndi mtsogoleri wa ophunzira.

Iwo anati bungwe lawo limadikila lipotili kuti alondoleze nkhaniyi.