A bungwe anangotinyenga – atelo ophunzira a ku Chanco

Advertisement
Chanco

Ophunzira a ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor ati bungwe loona za ufulu la HRCC linangowanyenga basi.

Ophunzira a ku sukuluyi anena izi patatha chaka bungwe lomenyela ufulu ili litalonjeza kuti lifufuza nkhanza za Apolisi zomwe anachitila asungwana a pa sukuluyi.

Pa zionetselo za chaka chatha zomwe ophunzira pa sukuluyi adachita pofuna kuti ndalama zomwe amalipila zitsike, Apolisi anajambulidwa akuswa makofi atsikana awiri a pa sukulupo.

Zitachitika izo, a bungwe la HRCC analonjeza kuti afufuza nkhaniyi koma kufika lero ati kuli chete.

“Kukhala ngati zinali ntchetela zoti afufuza zija chifukwa kufika lero kuli ziii. Anatipaka phula m’maso basi amene aja,” anatelo a Ayuba James amene ndi mtsogoleri wa ophunzira.

Iwo anati bungwe lawo limadikila lipotili kuti alondoleze nkhaniyi.

Advertisement

17 Comments

  1. Zopusa basi, munatupa ndikudya nandolo kumudzi. Mmalo moti musekelele kuti mwayamba kudyanso soseji Mumvekere a HRCC anatinyenga opanda kondomu!!!! za zii basi. Munaswedwa munaswedwa basi. Kodi inu mumaziwona ngati nadani anthu ophunzira Chichewa mmalo mwa sayansi? Bwanji sitimva zopusa kuchokera ku CoM, Luanar, Mzuni and MUST?

  2. you want to learn? Or school close? Or continuing the past issues???…
    Kod mesa inunso Apolice munawachita khaza powagendaa???
    shut up chancellor College!!!,Dont give the country headache all the tym! just celebrate re-opening of ur academic or continuing the past issues and stay home…

Comments are closed.