Nduna zonse zopanga u Chaponda zinyetsedwa – APM

Advertisement
George Chaponda with Peter Mutharika

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika auza nduna zonse zatsopano kuti saziteteza ngati zikhale ndi dyela pa chuma.

Polankhula ku nyumba ya boma ku Lilongwe kumene kunali mwambo olumbilitsa nduna zinayi zatsopano, a Mutharika ananena kuti iwo sakusekelela katangale.

“Nduna zonse zochita katangale ndizichotsa ndi kuzisiya kuti zithane ndi lamulo,” anatelo a Mutharika.

 Peter Mutharika
Mutharika (Kumanja) Wachenjeza nduna zake

Iye anati sakufuna nduna zokhetsa dobvu zikaona ndalama koma akufuna zolimbika ntchito ndi zokumva malangizo.

“Ine ndikufuna nduna za khama pa ntchito ndi zokumva malangizo a ena,” anatelo a Mutharika.

Mawu a Mutharika akubwera nduna yakale yoona za ulimi a George Chaponda atanjatidwa ndi Apolisi poganizilidwa kuti anachita za katangale.

Anthu ambiri anadabwa kuti kwa nthawi yoyamba, mtsogoleri anakanika kuteteza nduna yake.

Pa nduna zimene zinalumbila dzulo panali Mayi Anna Kachikho ndi a Aggrey Massi.