Bambo wadzipha atatopa ndikudwazika mkazi wake

Advertisement
Kasungu

Zina ukamva kamba anga mwala, bambo wina wazaka 81 ku Kasungu waphwanya lonjezo la paukwati lokhala limodzi ndi mkazi wake pamavuto ndi pa mtendere pomwe.

Malingana ndi malipoti a apolisi, bamboyu yemwe dzina lake ndi Symon Chirwa anapezeka atadzikhweza lachiwiri m’boma la Kasungu kamba kotopa ndikudwazika mkazi wake.

Apolisi ati auzidwa kuti mkazi wa malemuyu ndiodwalika ndipo pano pakutha zaka zitatu chimuyambileni matenda koma sakupezabe bwino.

Izi zakhala zikudandaulitsa bambo Chirwa omwe anafika pouza abale awo kuti atopa ndikusamalira matendawa.

A Chirwa amauza anthu owayandikira kuti zakhala zikuwapweteka kuti udindo onse unali m’manja mwawo.

Iwo amati chimawawawa kwambiri ndichoti iwo omwewo aziphika, kutsuka mbale, kuchapa zovala zawo ndi za akazawo komaso kuweta ng’ombe.

A Chirwa amati izi zimawatopetsa kwambiri poganiziraso kuti ana awo onse palibe ndi m’modzi yemwe amene amawathangatira pa ntchito zonsezo.

Ndipo pofuna kusiyana ndi zonsezi, A Chirwa anazikhweza m’mawa wa lachiwiri.

A polisi ati mwana wina wa zaka zisanu ndichimodzi (6) yemwe amafuna kukatunga madzi pachitsime china ndiyemwe anapeza thupi la malemuwa likulendewera kumtengo m’munda wina oyandikana ndi nyumba ya malemuwa ndipo anathamanga kukadziwitsa anthu za nkhaniyi.

Padakali pano a polisi ati sakuganizira zauchifwamba zilizonse pankhaniyi ndipo ati zotsatira zakuchipatala zomwe madotolo apeza atapima thupi la malemuwa zaonetsa kut imfa ya a Chirwa inali kamba kopotokoledwa khosi ndiso kobanika.

A Chirwa ankachokera m’mudzi wa Mwalimu mfumu yaikuli Kaluluma m’boma la Kasungu.