Bambo wadzipha atatopa ndikudwazika mkazi wake

96

Zina ukamva kamba anga mwala, bambo wina wazaka 81 ku Kasungu waphwanya lonjezo la paukwati lokhala limodzi ndi mkazi wake pamavuto ndi pa mtendere pomwe.

Malingana ndi malipoti a apolisi, bamboyu yemwe dzina lake ndi Symon Chirwa anapezeka atadzikhweza lachiwiri m’boma la Kasungu kamba kotopa ndikudwazika mkazi wake.

Apolisi ati auzidwa kuti mkazi wa malemuyu ndiodwalika ndipo pano pakutha zaka zitatu chimuyambileni matenda koma sakupezabe bwino.

Izi zakhala zikudandaulitsa bambo Chirwa omwe anafika pouza abale awo kuti atopa ndikusamalira matendawa.

A Chirwa amauza anthu owayandikira kuti zakhala zikuwapweteka kuti udindo onse unali m’manja mwawo.

Iwo amati chimawawawa kwambiri ndichoti iwo omwewo aziphika, kutsuka mbale, kuchapa zovala zawo ndi za akazawo komaso kuweta ng’ombe.

A Chirwa amati izi zimawatopetsa kwambiri poganiziraso kuti ana awo onse palibe ndi m’modzi yemwe amene amawathangatira pa ntchito zonsezo.

Ndipo pofuna kusiyana ndi zonsezi, A Chirwa anazikhweza m’mawa wa lachiwiri.

A polisi ati mwana wina wa zaka zisanu ndichimodzi (6) yemwe amafuna kukatunga madzi pachitsime china ndiyemwe anapeza thupi la malemuwa likulendewera kumtengo m’munda wina oyandikana ndi nyumba ya malemuwa ndipo anathamanga kukadziwitsa anthu za nkhaniyi.

Padakali pano a polisi ati sakuganizira zauchifwamba zilizonse pankhaniyi ndipo ati zotsatira zakuchipatala zomwe madotolo apeza atapima thupi la malemuwa zaonetsa kut imfa ya a Chirwa inali kamba kopotokoledwa khosi ndiso kobanika.

A Chirwa ankachokera m’mudzi wa Mwalimu mfumu yaikuli Kaluluma m’boma la Kasungu.

Share.

96 Comments

  1. Ngati afera maganizo amadam ambili anthu akanafa munjira yomweyo.aliyese amakumana nimavuto kwabwino mkulimba mtima, mulungu samamukhulupilira amapembeza mafano.aziwona okha komwe ali

  2. kodi munthu akamwalira ndi uchimo,mzimu wake umapita directly ku Gehena kapena Gehena idzasunga mizimu ya ochimwa after judgement?assist me plz,amene mukulemba kuti RIG

  3. Good day my friends I am so happy to share my great testimony to my friends on Facebook and Twitter all over the world I was a HIV patients for 6 year my friend introduce me to DR ABUMEN who cure me from the deadly virus I am now negative now I am a living testimony if you are affected with this virus because when u keep silent the virus will eat you up, You can also email him for any kind of help via email ([email protected]) or whatsapp him on +2347085071418.

  4. Sunganeneletu kt ndiwoyipa mpaka Mulungu atadzaweluza,sikudziwa kukula kwa chikhulupiliro chake.Bamboyu wafa chifukwa cha mkazi.Ngochepa amafa kamba ka munthu wina,ambirife timayendela mau oti kufa safelana.

  5. Mwina anaona kuti mkaziyo sangacìre ndiye kamba kacisoni ndi cikondi sanafune kuona mkaziwake akuthata ndi imfa anangoganiza zoti atsogole.koma gogoyu analibe ana akuluakulu?matendawo amadwalitsadi yekha?pali chomwe cìkubitsidwa pankhaniyi mwina akucìkazi amamunena mkuluyu kuti mfiti nde anangozipha

  6. apo ndipovuta dipo nd zachison kwambili koma panthaw yomwe amanena kwa abale awo za nkhan ya kutopai. amawathandiza motan? nanga abale awo a amaiwo ose anatha kumwalila? nanga abale awo amalemuyi kulibe anthu amzelu ? oti akanat amalumewa atopadi iwe mtsikana pita uzikawatungila madzi apa abale ose ambali ziwili ose nd olakwa chifukwa zaka zitatu ekha ku ntchito mmmmm munthuyu anatopad maka ci mayendawo ayi koma zochitika za akuchikaz kapena tinene kut bamboyu nd oipa ku mbali zonsezo?

  7. Happiness is all am experiencing now as am posting this about Dr Abuu the man that God has been using to heal people, and I and my Husband are one of them because we are cured from hiv/aids by his medicine, if not for God and Dr Abuu my children would have been orphans today but i thank God and Dr Abuu for saving my life, for those who are passing through the same should call or whatsapp Dr Abuu on whatsapp with his number +2348066454364 OR EMAIL [email protected]

  8. pamenepatu ngati mutadekha bwino bwino ndikulingalira m’mene amazuzikila mkuluyu mukhoza kundibvomeleza kuti ana ake ndiwoyipa kwambiri ndipo ndiwomwe amuphetsa m’dalayu

%d bloggers like this: