Nyetsani aphungu onse akuba ndalama za chitukuko – alipempha boma

Advertisement
Parliament

Aphungu onse amene anatalikitsila manja awo okonda kusololasolola mu ndalama za boma akuyenela kupeza mavuto.

Malinga ndi katswiri pa nkhani za ndale ndi kayendetsedwe ka boma, a Wonderful Mkhutche, Boma lisanyengelele mbava zonse za aphungu.

“Tikudziwa ku Malawi kuno chilungamo chimavuta koma pa nkhani iyi yokha a boma asayang’ane mbali,” anatelo a Mkhutche.

Iwo anaonjezelapo kunena kuti aphungu onse amene akuganizilidwa kuti ananyambita ndalama za chitukuko za ku dera kwawo afufuzidwe ndipo apititsidwe ku bwalo la Milandu.

“Akapezeka olakwa, chonde lamulo ligwile ntchito,” anatelo a Mkhutche.

Iwo anapemphanso a Malawi kuti asiye kusankha anthu akuba mu maudindo.

“Nawo anthu azisankha anthu a khalidwe labwino, a kamberembere awa kumawasiya,” iwo anatelo.

Nduna ya zachuma a Goodall Gondwe anaulula mu nyumba ya malamulo kuti ndalama ya chitukuko cha mu dera simagwila ntchito yake. Ati ena mwa aphunguwo amaipanga phwando.

Bungwe lolimbana ndi katangale la ACB lanena kuti likufuna liyambe kufufuza aphunguwo.