Nyetsani aphungu onse akuba ndalama za chitukuko – alipempha boma

32

Aphungu onse amene anatalikitsila manja awo okonda kusololasolola mu ndalama za boma akuyenela kupeza mavuto.

Malinga ndi katswiri pa nkhani za ndale ndi kayendetsedwe ka boma, a Wonderful Mkhutche, Boma lisanyengelele mbava zonse za aphungu.

“Tikudziwa ku Malawi kuno chilungamo chimavuta koma pa nkhani iyi yokha a boma asayang’ane mbali,” anatelo a Mkhutche.

Iwo anaonjezelapo kunena kuti aphungu onse amene akuganizilidwa kuti ananyambita ndalama za chitukuko za ku dera kwawo afufuzidwe ndipo apititsidwe ku bwalo la Milandu.

“Akapezeka olakwa, chonde lamulo ligwile ntchito,” anatelo a Mkhutche.

Iwo anapemphanso a Malawi kuti asiye kusankha anthu akuba mu maudindo.

“Nawo anthu azisankha anthu a khalidwe labwino, a kamberembere awa kumawasiya,” iwo anatelo.

Nduna ya zachuma a Goodall Gondwe anaulula mu nyumba ya malamulo kuti ndalama ya chitukuko cha mu dera simagwila ntchito yake. Ati ena mwa aphunguwo amaipanga phwando.

Bungwe lolimbana ndi katangale la ACB lanena kuti likufuna liyambe kufufuza aphunguwo.

Share.

32 Comments

  1. Ngodya yoyamba ndipo yofunika m’boma la DPP ndi kuba , palibe amene watsala osaba koma kulengeza mabodza othana anchitidwe oipa kumbali akumauza bola thaiming’itu…osagwidwa NDE mukuti chani APA.

  2. Kkkk Guyz Mutakhala Inu Imadya Pamene Ayimangilira Masiku Chilungamo Chinatha Asiyen Ndi Nthaw Yawo Mwana Wankhuku Amawonera Make Kunyera Pogona Ndiye Mumat Awa Apanga Bwanj Pakut Amalaw Tinadziwa Ndi Mbiri Yakuba Ivn Azungu Amadziwa Ku England

    • You see how stupid you’re? How can Malawi be developed with such poor mindset? Some times I wish I was born somewhere else than Malawi…..I hope one day u will be out from bush called Malawi and see how people live outside Malawi..even Rwanda is much better than Malawi yet they had civil 1994.

  3. Vuto ndi m’tsogoleli wadziko lino kukonda kumbeleka akubawo ngati amachita kuwatuma, Chaponda pano akungokhala osamuyimba mu mlandu pamene ndi mbava yowonekelatu,

%d bloggers like this: