Atuluka ngati Maule mu Airtel Top 8: Malawi ikubwera chimanjamanja ku COSAFA

Advertisement
Malawi

Angopata ma pointi awiri okha, chigoli olo chimodzi sanamwetse.

Timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino lero yatuluka mu chikho cha mpikisano wa COSAFA umene ukuchitikila mu dziko la South Africa.

Malawi
Yatuluka mu Cosafa osagoletsako olo chigoli chimodzi.

Malawi yatuluka itakanikana ndi timu ya anyamata a chichepele a Angola.

Mu masewero oyamba, timu ya dziko lino idakumana ndi anyamata a Magufuli amene anagoleka zigoli ziwiri kuwasiya a Malawi kukamwa pululu atalephela kumwetsa olo chimodzi.

Masewero a Malawi achiwiri adasewela ndi timu ya Mauritius ndipo mbali zonse ziwiri palibe anaona golo la mzake.

Mu masewero ake otsiliza, Malawi inakumana ndi Angola koma golo osaliona. Nawo a Angola chimodzimodzi.

Malawi imafunika kugonjetsa Angola ndinso Mauritius igonjetse Tanzania kuti timu ya dziko linoyi ipitilile.

Padakali pano anyamata amenewa akuyembekezeka kubwela kumudzi.