Zophana podula mutu zayamba kuchulukira ku Malawi

Advertisement
blood

Munthu wa umunthu amakhala ndi chisoni, mantha, ulemu mwa zina koma izi sizili choncho m’dziko muno pamene mchitidwe ophana ukupitilira.

Izi zikutsimikizika pamene bambo wina wa zaka 67 ku Nkhatabay wapezeka ataphedwa ndikudulidwa mutu komanso ziwalo zobisika.

Malingana ndi a polisi m’bomali, ophedwayo ndi a Sikunyala Mnyimbiri omwe thupi lawo lapezeka m’dera la Msakanene m’boma lomwelo la Nkhatabay.

Ofalitsa nkhani za a polisi m’bomali Ignatius Esau ati a Mnyimbiri omwe amakhala okha anapezeka atafa pa 10 May ndipo thupi lawo linapezeka m’munda wina otalikirana ma malipande 15 kuchokera pa nyumba yawo.

A Esau ati okuphawo adadula mutu ndi ziwalo zobisika za a Mnyimbiri, ndipo a chipatala adati imfa yawo inadza kamba kodulidwa mutu.

Panakali pano, a polisi apempha aliyense amene angakhale ndi uthenga uliwonse omwe ungathandize a polisi kudziwa za omwe adapanga chipongwe a Mnyimbiri kuti awatsine khutu.

A Sikunyala Mnyimbiri adali ochokera m’mudzi mwa Nthulinga mfumu yaikulu Timbiri m’boma lomweli la Nkhatabay.

Izi zadza patangotha pafupifupi ma sabata anayi anthu enanso atatu a banja limodzi, amayi, abambo ndi mwana, omwe adapita kukagula galimoto loyendera ku Lilongwe atapezeka ataphedwa ndikudulidwa mitu yawo.

Matupi a atatuwa adapezeka mu nkhalango ya Bunda mu mzindawu.