Zophana podula mutu zayamba kuchulukira ku Malawi

37

Munthu wa umunthu amakhala ndi chisoni, mantha, ulemu mwa zina koma izi sizili choncho m’dziko muno pamene mchitidwe ophana ukupitilira.

Izi zikutsimikizika pamene bambo wina wa zaka 67 ku Nkhatabay wapezeka ataphedwa ndikudulidwa mutu komanso ziwalo zobisika.

Malingana ndi a polisi m’bomali, ophedwayo ndi a Sikunyala Mnyimbiri omwe thupi lawo lapezeka m’dera la Msakanene m’boma lomwelo la Nkhatabay.

Ofalitsa nkhani za a polisi m’bomali Ignatius Esau ati a Mnyimbiri omwe amakhala okha anapezeka atafa pa 10 May ndipo thupi lawo linapezeka m’munda wina otalikirana ma malipande 15 kuchokera pa nyumba yawo.

A Esau ati okuphawo adadula mutu ndi ziwalo zobisika za a Mnyimbiri, ndipo a chipatala adati imfa yawo inadza kamba kodulidwa mutu.

Panakali pano, a polisi apempha aliyense amene angakhale ndi uthenga uliwonse omwe ungathandize a polisi kudziwa za omwe adapanga chipongwe a Mnyimbiri kuti awatsine khutu.

A Sikunyala Mnyimbiri adali ochokera m’mudzi mwa Nthulinga mfumu yaikulu Timbiri m’boma lomweli la Nkhatabay.

Izi zadza patangotha pafupifupi ma sabata anayi anthu enanso atatu a banja limodzi, amayi, abambo ndi mwana, omwe adapita kukagula galimoto loyendera ku Lilongwe atapezeka ataphedwa ndikudulidwa mitu yawo.

Matupi a atatuwa adapezeka mu nkhalango ya Bunda mu mzindawu.

Share.

37 Comments

  1. Ikutheka ndiimeneyi yophanayi zina zonse zikukanika iiiiiiii Malawi ndi pambali penipeni.Satana wapezako kuyanja basi,akuyenda wapansi now days.

  2. We have more organizations like human rights, whr are they while pipo are being killed like goats. Wake up and tell the government to increase the sentence for that pipo.

  3. Osadandaula za kudula mutu ai koma kuphana,chifukwa kupha kwabwino mkudula mutu ndiye ngati munthu waphedwa ngakhale asadulidwe mutu waphedwa basi

  4. Kuipa kochiluka ama CHINA ndikumeneko akupanga mang’ina makamaka mutu nambala wani .ndiye ndidani abwelesa ma chana Ku Malawi kuno MCP,UDF,PP olo DPP

  5. Abale tingotaya nthawi ndimanyozana koma eni akefe tiyenela kuchitapo kanthu.Tikawa dziwa anthu amene akupanga zoopsazi nafenso tiyenela kupha zigawengazi komanso ma Mp apange lamulo lakuti yemwe wapha m,nzake nayenso aphedwe.Tiyenela kuziwa kuti zonse zophanazi zabwela ndi matipate kale panthawi yakamuzu kuyenda mbulanda,kubela mayeso,ziphuphu ndi katangale komanso zophana kudalibe.

  6. Abale tingotaya nthawi ndimanyozana koma eni akefe tiyenela kuchitapo kanthu.Tikawa dziwa anthu amene akupanga zoopsazi nafenso tiyenela kupha zigawengazi komanso ma Mp apange lamulo lakuti yemwe wapha m,nzake nayenso aphedwe.Tiyenela kuziwa kuti zonse zophanazi zabwela ndi matipate kale panthawi yakamuzu kuyenda mbulanda,kubela mayeso,ziphuphu ndi katangale komanso zophana kudalibe.

  7. ma MP ndi amene akupanga zimenezo komanso anthu amabizinesi nchifukwa mukuwona zikupitilila ngati ndikunama tsusani koma olo munene uchifwamba suzatha chifukwa mabwana ambili akupanga zimenezo olo ma albino akuphedwa chifukwa cha anthu amenewa ma MP ndi akuluakulu a ma buzinesi

  8. Macomment anuanthuenanu ndiopanda nzelu inundine tiyenela kugwilanamaja ndikupangacimozi amend mukuwanyozawo sangaziwe anthuamene akupangazacipogwewo pondainu ndiine inumumawaziwa koma simucitapo katha aliyetse akhale mulonda wanzake

  9. Koma Guyz Dziko likupita kuti? ndipo mukamapanga zoopsa zanuzo umunthu mumakhala mutausiya kuti? MULUNGU ADziwe nanu chochita ndipo asakusiyeni choncho ndipo ndikukhulupilila kuti posachedwapa Mukhala mutafika pothela paulendo wanu. MULUNGU Sangalole kuti inu muzikhala mmene mukuchitilamo kuononga anthu ake.

  10. Security lapse under DPP.The responsible minister is pheee in her office. Milomo psuu uku akugeya anyezi wa Boma.Khosi sololoke ngati nkhuku yodya gaga yekhayekha uku a malawi akutha!za ziii!Stupid!

%d bloggers like this: