Mbava zithyola Polisi

Advertisement

Mbava zathyola ndi kuba pa polisi yaying’ono ya Chimbiya m’boma la Dedza.

Nkhaniyi ikuti mbavazi zinakaba pa polisiyi nthawi yomwe wapolisi amagwila ntchito yoyang’anila anapita kukakhala nawo pamalo ochitila chipikisheni.

Mbavazi zomwe sizikuziwika zinakwanisa kuba mifuti iwiri ndi zipolopolo zake mu chipinda chosungila katundu.
Katundu yemwe anabedwa ndi monga zidindo, galasi la sola, mpando wa mu ofesi, ndi makina opanila mapepala.

Pakali pano apolisi sanamange munthu aliyese kutsatila kuchitika kwa nkhaniyi.

Iwo ati akufufuza kuti apeze uyo yemwe waba kupolisiyi.