Maiko a Malawi ndi Tanzania akhazikitsa mwezi wa December chaka chino ngati mathero a zokambirana zokhudza mkangano wolimbirana malire a nyanja ya Malawi.
Nduna yoona zaubale wadziko lino ndi maiko ena, a Francis Kasaila, ndiyo yonena izi polankhula ndi Malawi24.
Malingana ndi a Kasaila, wapampando wa komiti yapadera yomwe ikumva zankhaniyi yemwenso ndi mtsogoleri wakale wa dziko la Mozambique a Joaquim Chissano wati wavomereza za panganoli.
A Kasaila ati a Chissano atsikimiza kuti nthumwi zikhala zikutsiliza kukonzekera zokambirana pompano.
“Mgwirizano umene unachitika pakati pamapulezidenti athu awiri, Professor Arthur Peter Mutharika komanso Pulezidenti John Magufuli wa m’dziko la Tanzania, unali woti ife nduna za m’maiko awirife tilembe makalata kuwapempha atsogoleri amene akuyendetsa nkhani imeneyi kuti ntchito imeneyi idakachitika mwamsanga kuti ithepo.
“Zimenezi tachita, tawalembera kalata ndipo kalatayi itapita. Pakadali pano a komishona athu ku Maputo ali kalikiliki kutsatira nkhaniyi ndipo akhala akumana ndi a Joaquim Chissano kawiri konse kuti amve kuti zinthu zili pati.
“Ndiulule pano kuti iwo anditsikimizira kuti komiti iyesesa kuti zokambirana zonse za nkhani yolimbana nyanja ya Malawiyi ikhale nkhani ya makedzana pofika kumapeto a chaka chino,” anatero a Kasaila powuza wolemba nkhani wa Malawi24.
Maiko a Malawi ndi Tanzania, anagwirizana kumayambiliro a chaka chino kuti apemphe komitiyi kuti iyambenso ntchito yaumkhala pakati pazamalire a m’maikowa.