Madzi akwera mtengo

Advertisement
BWB

Kuyambira pa September 1 2024, ogula m’dziko muno akulipira pafupifupi 10 peresenti yowonjezera pa mtengo wa madzi omwe akugwiritsa ntchito pambuyo poti unduna wa zamadzi ndi ukhondo wavomereza kusintha kwa mitengoyi.

Malingana ndi chidziwitso chomwe boma latulutsa pa August 30, pafupifupi 10 peresenti ndi yomwe mabungwe a Blantyre Water Board (BWB), Lilongwe Water Board (LWB), Northern Region Water Board (NRWB), Central Region Water Board (CRWB) ndi Southern Region Water Board (SRWB) awonjezera pa mitengo yatsopanoyi.

Malipoti akusonyeza kuti BWB yasintha mtengo wake kuchoka pa 60 tambala kufika pa 66 tambala pa lita la madzi operekedwa kuchokera kumalo osungira madzi ammudzi kapena ma “kiosk” ndi kuchoka pa K1.59 kufika pa K1.75 pa lita limodzi pa malita 5,000 aliwonse ogwiritsa ntchito.

Mbali inayi, NRWB yakweza mtengo wa madzi operekedwa kuchokera kumalo osungira madzi ammudzi kuchoka pa K630 kufika pa K691 pa “cubic metre” ndiso kuchoka pa K1,830 kufika pa K2,009 pa “cubic metre” pa ntchito zapakhomo.

Nalo bungwe la LWB lakweza mtengowu kuchoka pa K3,456 kufika pa K3,802 pa “cubic metre” iliyose yogwiritsa ntchito zapakhomo, zonse zomwe zikuyimira pafupifupi 10 peresenti yowonjezeka. Komabe, LWB siinakweze mitengo ya madzi operekedwa kuchokera kumalo osungira madzi ammudzi.

Izi zikuchitika ngakhale kuti mlembi wamkulu wa unduna wa za madzi ndi ukhondo, Elias Chimulambe, adatsimikiza kuti anthu omwe amapeza ndalama zochepa sakhudzidwa ndi pempho loti mitengoyi ya madziyi ikwere.

Chaka chatha mabungwe asanu a madzi m’dziko muno adapempha kuti asinthe mitengo ya madzi pofuna kuonetsetsa kuti azikwanitsa kugwira Ntchito yawo bwino. Pempholi lidayimitsidwa kaye kamba koti anthu ambiri anali osakondwa ndi ganizoli.  

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.