Kugwa kwacha, kukwera kwa zipangizo za ulimi wa fodya kukupweteka alimi-watero Banda

Advertisement

A Chinoko Banda, yemwe ndi m’modzi mwa alimi omwe amalima komanso kugulitsa fodya, wadandaura kuti kukwera kwa zipangizo za ulimi wa fodya monga feteleza kamba kakugwa kwa kwacha, kwapangitsa kuti alimi  adzipeza phindu lochepa pa nthawi yogulitsa Fodya.

Banda wanena izi pamene President Lazarus Chakwera amatsegurira malonda a fodya ku msika wa Chinkhoma ku Kasungu.

‘Phindu silikuoneka mu ulimi wa Fodya’-Banda.

A Banda anati akhala akulima fodya kwa nthawi yaitali koma zaka zambuyomu, anasiya ulimiwu ataona kuti phindu  silikuoneka chifukwa choti amalowetsa ndalama zochuluka pa ulimiwu koma ikafika nthawi yokolora phindu limakhala lochepa.

Iwo anawonjezera ponena kuti kuyambira kale lonse, fodya wakhala ulimi opindura ndiponso odalilika chifukwa Iwo akwanitsa kuphunzitsa ana kuchokera mu ulimiwu.

Poyankhura ndi wapampando wogura fodya ku Kampani ya Nyasa Group, Konrad Buckle, anati iwo ndi osangalara kuti alimi akupitiliza kugulitsa fodya wabwino ku msika potengera kuti ndi fodya yekhayo wosamalilika bwino amene amagulitsidwa pa mtengo wabwino komanso sakanidwa pa msika.

‘Tigula Fodya wambiri chaka chino’- Buckle.

A Buckle ati Iwo ndi okonzeka kugura fodya wambiri chaka chino pofuna kulimbikitsa alimi kuti apitilize kulima fodya komanso kupereka mwayi kwa alimi ena omwe sanayambepo ulimiwu kuti ayambe.

Lero ngati tsiku losegura msika wa malonda a fodya,ma Belo 2,165 ndi omwe anapititsidwa   ku msikawu kuti aguritsidwe. Msika wa Chinkhoma  umagulitsa ma Belo okwana 5,000 pa tsiku liri lonse. Fodya wabwino kwambiri amugula pa mtengo wa 3 dollar 1 centi  pomwe fodya wotsika kwambiri ali pa 2 dollar 20 cents.

Ma Kampani ngati Limbe leaf Tobacco Company , Alliance One Tobacco Malawi, JTI, Premium Tobacco Malawi Ltd, African Tobacco Services, Associated Central African Ltd, Watergen, Voedsel, Hail and Cotton ndi Nyasa Manufacturing Company, ndi omwe ndi ovomelezedwa kugula fodya.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.