M’busa atsindika malemba molakwika pa mwana wa zaka 16

Advertisement
Lilongwe Police

Apolisi kwa Mpingu m’boma la Lilongwe akusunga mchitolokosi mbusa wa mpingo wa Kadziyo Disciples, a Mccrystal Charlie a zaka 56, chifukwa chogonana ndi kuchimwitsa mtsikana wa zaka 16.

Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi ku Lilongwe a Hastings Chigalu, abusawa adagwa nalo mchikondi buthuli m’mwezi wa May chaka chatha pomwe limabwerabwera kudzatunga madzi pa m’jingo wa kachisi.

Mwezi wa December chaka chatha buthuli lidaima ndipo agogo ake atampanikiza adaulura kuti mwini chonyamulidwacho ndi abusa a Charlie.

Malinga ndi a Chigalu zotsatira za ku chipatala zinawonetsa kuti mtsikanayu ali ndi mimba ya ma sabata 21.

“M’busayu yemwe adalekana ndi mkazi wake anawuza apolisi kuti adagwirizana zokwatirana ndi mtsikanayu zitadziwika kuti ali ndi pakati, koma achibale adakana nkhani ya banja pokhudzidwa ndi zaka za mtsikanayu apo ndi pamene apolisi analowelera,” anatero a Chigalu.

Abusa a Charlie omwe ndi ochokera m’mudzi mwa a Chilembwe kwa mfumu yayikulu Tengani m’boma la Nsanje, akawonekera ku bwalo la milandu kuyankha mlandu ogonana ndi mwana.