Bon kalindo wati DPP yapanga khalidwe lonunkha ku Ndirande

Advertisement
Bon Kalindo

M’modzi mwa omenyera ufulu wa anthu mdziko muno a Bon Kalindo ati zomwe anayankhula akuluakulu ena a chipani cha Democratic Progressive (DPP) ku msonkhano wa ndale ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre ndi zokolezera udani komanso ndi khalidwe lonunkha pamene nkhondo yolimbana ndi udani ndi nkhanza pa ndale ili mkati.

Poyankhula mu uthenga wawo omwe amatulutsa tsiku lililonse a Kalindo agundako zomwe phungu wa DPP ku Mulanje Bale a Victor Musowa adanena lamulungu pa nsonkhano wa ndale.A Kalindo ati akuluakulu a DPP akhala akudzudzula chipani cha MCP limodzi ndi akuluakulu a polisi polekelera khalidwe la nkhanza pa nthawi ya ziwonetselo, misonkhano ya ndale ndi zina koma iwo ngati chipani cha DPP akhalanso patsogolo kulimbikitsa nkhanza.

Iwo ati chipani cha DPP chimayenera kukhala chitsanzo chabwino polimbikitsa mtendere osati kukolezera udani pa zipani komanso kudulirana malire pa ndale m’malo mongokamba mfundo zawo kwa anthu pa misonkhano yake.A Kalindo ati DPP isaphe ufulu wa demokalase mdziko muno ponena kuti zikhonza kubweretsa nkhondo ndi zipolowe mdziko.

Lamulungu a Victor Musowa adalankhula kwa anthu kuti asamvere komanso kumulora munthu wina aliyense amene angabwere kudzakamba za “Kwacha’ umene ndi mkuwe wa chipani cha MCP.

M’neneli wa chipani cha DPP a Shadreck Namalomba alankhula ndi wailesi ina kuti zomwe analankhula a Musowa sizikukhudza chipani koma kuti adali maganizo awo a Musowa ndipo anati zotelezi sizoloredwa mu chipanichi.

Anthu ena ati a Musowa akuyenera kubweza mawu amene analankhula ku Ndirande ndipo akuyenera kupepesa ku mtundu wa aMalawi Polankhula mawu omwe ali ndi kuthekera kobweretsa ndi kukolezera chisokonezo pamene dziko likuyandikira kuponya masankho osankha mtsogoleri wa dziko, aphungu ndi ma khansala pa 16 September chaka chamawa.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.