Malawi akulowera ku chigwembe – Kafukufuku

Advertisement
Afrobarometer

…DPP idzapambana pa masankho…

Malinga ndi kafukufuku wa AFRO-Barometer yemwe wavumbuluka pa 06 December wawonetsa kuti Malawi akuyenda mchizilezile ndipo akulowera kolakwika.

Malinga ndi kafukufuyu anthu 76 pa handede aliwonse (76%) afotokoza kuti Malawi akulowera kolakwika kulekana ndi anthu 22 pa handede aliwonse (22%) omwe anena kuti Malawi akulowera njira yabwino.

Kafukufuyu wawonetsanso kuti boma la a Lazarus Chakwera lakanika kugwira mitengo ya katundu pamene anthu anayi pa handede aliwonse (4%) ndi omwe ati boma lagwira bwino mitengo ya katundu.

Richard Chimwendo Banda
Chimwendo Banda: Boma ndilomweli.

Kafukufuyu wawuluranso kuti anthu akanaponya voti yosankha mtsogoleri wa dziko pa nthawiyi DPP ndi yomwe imapambana ndi 43% kutsatirana ndi MCP 29%, UTM 7%.

Zadziwikanso kudzera mu kafukufuluyu kuti nkhondo yolimbana ndi katangale ndi ziphuphu idakali chinthu chovuta kuchigonjetsa pamene zaonetsa kuti boma silikuchita bwino polimbana ndi katangale pomwe 9% yokha ya anthu ndi yomwe yati nkhondoyi yumenyedwa bwino.

Polankhula ndi atolankhani, mlembi wa chipani cha Malawi Congress MCP, a Richard Chimwendo Banda ati iwo sakuchoka m’boma ponena kuti kafukufuku wa AFRO-Barometer wakhala akuphonyapo m’mbuyomu.

A Chimwendo ati kafukufuku wa AFRO-Barometer adachitika pa nthawi imene zinthu m’dziko muno sizinali bwino kwenikweni.

“Pano DPP inagawanika patatu ena anakayambitsa zipani zawo ndipo pano mavuto omwe analipo akukonzedwa ndipo anthu ambiri akufuna boma ili lipitilizebe, palibe angalole DPP kubweleranso m’boma anthu anavutika nthawi ya DPP,” anatero a Chimwendo.

Akatswiri pa nkhani zandale ati atsogoleri a ndale amadana ndi zotsatira za kafukufuku zikakhala sizikuwakomera.

AFRO-Barometer ndi kafukufuku amene amachitika ndi mgwirizano wa mabungwe angapo mu Africa, ndipo ku Malawi kuno inachita ndi University of Malawi Centre for Social Research, ndipo linafunsa anthu 1200 m’mwezi wa August 2024, ndipo mayankho awo anayimira anthu ochuluka m’malawi muno.