Atakhala kwa kanthawi osatulutsa mawu oyikira kumbuyo utsogoleri omwe ulipowu mwachindunji komanso tsogolo la chomwe akufuna, wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Michael Usi lero abwera poyera kuwatsimikizira anthu za ubwino waboma ndi utsogoleri omwe ulipo pano wa a Lazarus Chakwera.
A Usi Alankhula lero ku Mwanza komwe anakumana ndi anthu komanso mafumu powamemeza kuti akalembetse, iwo atsimikiza kuti utsogoleri sumafunika kudukiza-dukiza ndipo kuti zitukuko zomwe zikuchitika pakali pano zipitilire iwo akhale akuwuza anthu munthu oyenera kuti adzamvotere kuti apitilize kulamula.
“Ulamuliro sumafunika kudukizadukiza, kuti zitukuko zomwe zikuchitikazi zipitilire, boma ndi lomweli,” anatelo a Usi.
A Usi omwe anali mtsogoleri wa UTM ati zina mwa zomwe zinakanika kukwanilitsika mu ulamuliro uno monga kudya katatu ndi chifukwa cha mavuto ambiri amene akhudza dziko lapansi.
A Michael Usi omwe sanakayime nawo pa mpikisano osankha atsogoleri a chipani chawo ponena kuti ndalama yopikisanilana yokwana 20 miliyoni kwacha inali yambirii yoti bola angothandizira anthu.