MRA iyamba kugwiritsa ntchito tindege ting’ono ting’ono pothetsa ukamberembere ozembetsa katundu

Advertisement
MRA

Bungwe lotolera misonkho m’dziko muno la Malawi Revenue Authority (MRA) lati posachedwapa liyamba kugwiritsa ntchito tindege ting’ono ting’ono (drone) m’malire a dziko lino pofuna kuthana ndi anthu omwe amazembetsa katundu osiyanasiyana.

M’modzi mwa akuluakulu a Bungweli, Dorothy Mataya, wananena izi lachiwiri sabata ino munzinda wa Mzuzu pomwe bungweli linakozera atolankhani maphunziro okhudza kutolera misinkho.

Mataya wati ndegezi zidziwuluka m’malire onse a dziko liko pofuna kuthetsa mchitidwe wozembetsa katundu pofuna kuthawa kupeleka misonkho.

Iye wati, “Mayiko ena akugwiritsa ntchito kwambiri ndegezi m’malire ake pothana ndi anthu omwe amazembetsa katundu.”

Mataya watiso MRA ikuyika zidindo (Stamp) pa katundu wina yemwe amalowa m’dziko muno zomwe ati zithandiza kuteteza aMalawi kumwa za kumwa zomwe zili ndikuthekera kuika miyoyo yawo pa chiswe.

Kudzera pa maphunzirowa, atolankhani alimbikitsidwa kuti adziwitse anthu ena za ubwino wopeleka misonkho pa zinthu zonse zomwe zimachokera kunja ndi momwe kuzembetsa katunduyu kukukhudzira chitukuko cha dziko lino.

Advertisement

One Comment

  1. The Government should figure out on how to grow a competitive production to reduce import and improve its export. not overtaxing its poor people who are trying to make ends meet.

Comments are closed.