Bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) kudzera mwa wa pa mpando wake a Annabel Mtalimanja atsindika kuti chiphaso cha unzika chokha ndi chomwe chimuyeneleze munthu kuti alembetse mu kawundula wa chisankho cha mchaka cha 2025 ndipo ati likhazikitsa chisankhochi pa 2 August 2024.
Poyankhula pa msonkhano wa atolankhani ku Lilongwe, a Mtalimanja ati chifukwa choti bungweli lidagawanso ma dela a aphungu bungweli likuyembekezeleka kuchitanso kalembera watsopano m’magawo atatu motsata malamulo ndipo ati akhale akufotokozera mtundu wa aMalawi m’masiku akudzawa. Iwo amema aMalawi omwe alibe chiphaso cha unzika kuti akalembetse.
Pa msonkhanowu bungwe la MEC lakhazikitsanso mutu omwe ndi mfundo yayikulu ya chisankho cha chaka chamawa (2025) omwe ndi “Kulimbikitsa utsogoleri wa demokalase ndi voti yanu”.
Wapampandoyu watsindikanso kuti anthu apewe kufalitsa nkhani zabodza zokhudxa chisankho ponena kuti zili ndi kuthekera kosokoneza zinthu zambiri ndipo ati anthu adalire uthenga ochokera ku bungweli komanso nyumba zofalitsa nkhani.
Dziko la Malawi likuyembekezeleka kudzaponya voti yosankha mtsogoleri wa dziko, aphungu ndi ma khansala pa 16 September 2025, ndipo tsikuli lidzakhala la tchuthi.