Nthambi Yoona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengo m’dziko muno yati Namondwe wotchedwa Filipo wafika m’dziko la Mozambique ndipo akuti apangitsa kuti madera ena m’dziko muno alandire mvula ya mphamvu.
Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe nthambiyi yatulutsa lero Lachiwiri chomwe chikusonyeza kuti namondwe wa Filipo wafika m’dziko la Mozambique m’mawa wa lero pa 12 March, 2024 pa gombe la kumwera kwa Beira mdzikolo.
Nthambiyi yati gombe la ku Beira komwe namondweyu wafikira, lili pa mtunda wotalika pafupifupi makilomita okwana 490 kuchokera ku Nsanje m’dziko muno ndipo akuti namondweyu yemwe wachokera mnyanja ya mchere ya India, sakhazikika malo amodzi.
Nthambiyi yati namondwe wotchedwa Filipo-yu apitiliza kuyenda kulowera kum’mwera kwa dziko la Mozambique ndipo akuyembekezeka kubwerela m’nyanja ya mchere ya India m’mawa wa Lachitatu pa 13 March, 2024.
Nthambi Yoona Zanyengo ndi Kusintha kwa Nyengoyi yawonjezera kuti pamene Namondweyu akupitiliza kulowera kum’mwera m’dziko la Mozambique adzilimbikitsabe mkumano wamphepo zochokera kumpoto chakumvuma ndi kumpoto chakunzambwe ndipo mvula yamphamvu ipitilirabe m’madera ena kumeneko komanso madera ena kuno makamaka amchigawo chakummwera.
Pakadali pano Nthambiyi yalangiza anthu mdziko muno kuti ayenera kukhala atcheru, makamaka m’madera omwe madzi amasefukira kawirikawiri komanso amphepete mwanyanja komanso kukhala motalikirana ndi mitsinje pomwe kukugwa mvula ya mphamvu chifukwa madzi akhoza kusefukira modzidzimutsa.
Kupatula apo nthambiyi yati makolo asalore ana awo kusewera m’malo akufupi ndi mitsinje, mu ngalande zodutsa madzi kapena madera osefukira madzi ndiposo atsatile machenjezo azanyengo ovomerezeka.