Mtsogoleri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers Thom Mpinganjira wachenjeza ochemelera timuyi makamaka aku Lilongwe pa nkhani yoyambitsa ziwawa, ndipo wati masewero aliwose aziyitanitsa apolisi okhala ndi mfuti kuti akathane ndi maliwongo aliyese.
Izi ndi malingana ndi kanema wina yemwe anthu akugawana pa masamba a nchezo yemwe akuwonetsa mpondamatikuyu akuyankhula za timu yawo ya Wanderers pa nkhani ya ziwawa zomwe ochemelera timu yovala makaka a ‘blue-yi’ anachita pa masewero ena chaka chatha.
Mtsogoleri wa timuyu wati ndiwokhumudwa komaso watopa ndi zindapusa zomwe timu ya Wanderers yakhala ikulandira kamba ka mchitidwe wa zipolowe pa masewero ena angapo ndipo wati tsopano wapeza njira zingapo zomwe akuti zipangitsa mchitidwewu kutheratu.
Mwazina, a Mpinganjira ati pa masewero aliwose omwe Noma idzisewera chaka chino, makamaka omwe adziseweredwera munzinda wa Lilongwe, iye ngati mkulu wa timu adziyitanitsa apolisi okhala ndi mfuti kuti azikakhazikitsa bata komaso kuthana ndi aliyese ofuna kuyambitsa chipwirikiti.
“Ku Lilongwe muwauze, ndizipanga hayala apolisi amfuti aja osati aja amangonyamura ndodo aja. Muwauze ma sapota a Wanderers ku Lilongwe, akangoyepekezaso, kukupita PMF, gemu (game) ili yose ya Wanderers ku Lilongwe ndizipanga hayala PMF ngati sakusamala,” wakalipa Mpinganjira.
Izi zikuchitika pomwe nkuluyu wathetsa ma komiti angapo atimu ya Wanderers pomwe akuchita chothekera kuti Noma iyambileso kumwa wankaka potsatira kulephera kutenga chikho chili chose mchaka cha 2023.
Chaka chatha timuyi inalipitsidwa chindapusa cha K22 million potsatira chipwirikiti chomwe chinachitika pa masewero ake ndi Silver Strikers pomwe ochemelera timuyi anawononga wina mwa katundu wa pa bwalo la masewero la Bingu ku Lilongwe kamba kosakondwa ndi chiganizo cha woyimbira Godfrey Nkhakananga.
Kupatula apo timuyi inalipitsidwaso chindapusa china kamba kolephera kusewera masewero achibwereza ndi Silver Strikers mumpikisano wa Airtel Top 8 komaso inapatsidwa chilango choti isatengeso nawo gawo mumpikisano uliwonse okozedwa ndi bungwe la FAM, koma mwa mwayi timuyi inakhululukidwa.