Zitasokonekera chaka chatha za ulendo wake obwera ku Mighty Mukuru Wanderers, Promise Kamwendo tsopano lero ndi osewera wa timuyi kutsatira mgwirizano wa zaka zitatu omwe atsimikizirana lero.
Mighty Mukuru Wanderers yatsimikiza za nkhaniyi kudzera mu zithunzi ndi uthenga omwe timuyi yatulutsa.
Kamwendo yemwe anali ku Premier bet Dedza Dynamos ngati osewera kutsogolo, koyamba anawonedwa akuwonetsa nawo chikho cha Castel challenge mu mzinda wa Blantyre masiku ochepa apitawa chomwe Wanderers idapata itagonjetsa Mzuzu city Hammers 1-0 ku Lilongwe.
Pa zaka zitatu zomwe Kamwendo wamenyera Dedza iyeyu wagoletsa zigoli 29 ndipo Wanderers yati ndi yokondwa ndi kubwera kwake popeza wabwera ku timuyi mgwirizano wake ndi Dedza utatha mphamvu.
Promise adakanika kupita ku Lali Lubani chaka chatha mgwirizano omwe unalipo ndi Wanderers utathetsedwa kutsatira kumang’ala komwe idachita FCB Nyasa Big Bullets ponena kuti adali atamaliza zonse za ndondomeko kuti Kamwendo akasewelere Bullets.